Zilengezo
◼ Mabuku amene adzagwiritsiridwa ntchito mu October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena a Nsanja ya Olonda kapena a magazini aŵiri onsewo. November: New World Translation of the Holy Scriptures ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. January: Lililonse la mabuku a masamba 192 otsatirawa amene mpingo ungakhale nawo m’sitoko pa chopereka cha 50t lililonse: Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu; Commentary on the Letter of James; Is the Bible Really the Word of God?; Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?; Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo; Life Does Have a Purpose; Mbiri Yabwino Yokusangalatsani ndi Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! MUSAODE alionse a mabuku ameneŵa m’Chingelezi ku Sosaite popeza kuti mulibe m’sitoko. Komabe, Sosaite ili ndi mtokoma wochepa wa buku la Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! m’Chicheŵa ndipo ameneŵa angaodedwe. Ngati mipingo ilibe alionse a mabuku otchulidwa pamwambapa m’sitoko, ingagaŵire Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Mphatika ya kope lino la Utumiki Wathu Waufumu ndiyo “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1995.” Iyenera kusungidwa kuti idzagwiritsiridwe ntchito m’chaka chonse cha 1995.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1995 pa oda yawo ya mabuku ya October. Timabukuto tidzapezeka m’Chicheŵa ndi Chingelezi. Kufikira pamene timabuku timeneti tidzakhalako ndipo maoda apangidwa, tidzasonyezedwa monga “Zoyembekezeredwa” pa mainvoisi a mpingo. Timabuku ta Kusanthula Malemba ndi zinthu zoodedwa mwapadera.