Thandizo Lenileni kwa Anthu Osauka
PAMENE Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anali padziko lapansi, anathandiza anthu osauka mofunitsitsadi. Pokambapo pa nkhani ya utumiki wa Yesu, mboni yoona ndi maso inati: “Akhungu alandira kuona kwawo, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphaŵi ulalikidwa uthenga wabwino.” (Mateyu 11:5) Komabe, bwanji za anthu osauka mamiliyoni ambirimbiri lerolino? Kodi pali uthenga wabwino uliwonse kwa anthu otere? Inde, pali uthenga wa chiyembekezo!
Ngakhale kuti anthu osauka nthaŵi zambiri amanyalanyazidwa ndiponso kuiwalidwa ndi anthu m’dzikoli, Mawu a Mulungu, Baibulo, amalonjeza kuti: “Sadzaiwalika nthaŵi zonse waumphaŵi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzawonongeka kosatha.” (Salmo 9:18) Mawu olimbikitsa ameneŵa adzakwaniritsidwa pamene Ufumu wa Mulungu, boma lenileni lakumwamba, lidzaloŵa mmalo ulamuliro wa anthu. (Danieli 2:44) Monga Mfumu ya boma lakumwamba limenelo, Yesu “adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”—Salmo 72:13, 14.
Kodi moyo udzakhala wotani pamene Kristu adzalamulira padziko lapansi? Amene adzalamuliridwa ndi Kristu adzapindula ndi ntchito yawo. Pa Mika 4:3, 4, Baibulo limati: “Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Ufumu wa Mulungu udzathetsa ngakhale matenda ndi imfa. (Yesaya 25:8) Limenelotu lidzakhala dziko labwino kwambiri! Tingakhulupirire malonjezo a m’Baibulo ameneŵa chifukwa ndi ouziridwa ndi Mulungu mwiniyo.
Kuwonjezera pa kupereka chiyembekezo, Baibulo limatithandiza kuti tithane ndi mavuto a tsiku ndi tsiku, monga mmene tingagonjetsere kudziona ngati osafunika, kumene kumabwera chifukwa chokhala osauka. Mkristu wosauka akamaphunzira Baibulo amadziŵa kuti ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu mofanana ndi Mkristu wolemera. Buku la m’Baibulo la Yobu limafotokoza za Mulungu kuti ‘sasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka, pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.’ (Yobu 34:19) Mulungu amakonda onsewo mofanana.—Machitidwe 10:34, 35.