Khirisimasi M’mayiko a Kummaŵa
• ZAKA MAZANA AŴIRI ZAPITAZO, katswiri wamaphunziro wotchuka kwambiri wa ku Korea anakacheza ku Peking, m’dziko la China. Poyang’anitsitsa chithunzi cholotchedwa kudenga la tchalitchi chachikulu, anaona kuti chinali cha Mariya atayangata khandalo Yesu m’manja mwake. Ponena za chithunzi chodabwitsa chimenechi iye anati:
“Mkaziyo anayangata mwana wonyentchera pamiyendo pake, wazaka pafupifupi zisanu kapena zisanu ndi chimodzi. Khosi la mkaziyu linali khoba, kuchita ngati sangalimbe mtima kumayang’anitsitsa mwana wake wamwamunayo kaamba komva naye chisoni chachikulu. Ndipo chakumbuyo kwawo kunali mizukwa yambirimbiri ndi ana okhala ndi mapiko akuuluka chapomwepo. Powayang’anitsitsa kutsindwiko, ankaoneka ngati andigwera nthaŵi ina iliyonse. Modabwa, ndinatambasula manja anga kuti ndaawakhe.”
ZIMENEZO zinachitika patapita nthaŵi yaitali pambuyo pa nyengo ya kukonzanso zinthu ya Reformation mu Ulaya, kale ndithu pambuyo pa nthaŵi yakusazindikira ya m’Nyengo Zapakati. Koma kwa anthu ambiri a Kummaŵa, Chikristu chinali chosadziŵika monganso mmene chithunzicho chinali. Mkhalidwewo wasinthadi tsopano! M’nyengo iliyonse ya Khirisimasi, zithunzi za Yesu ali wakhanda zimasonyezedwa. Mayiko a Kummaŵa azoloŵerana nazo kwambiri zithunzi zimenezo, ndipo misewu yambiri kumeneko yokhala ndi zokongoletsa za Khirisimasi tsopano ikufanana ndendende ndi ya ku Ulaya.
Madzulo a pa November 25, 1998, kutangotsala mwezi umodzi kuti tsiku la Khirisimasi lifike, msewu wa Champs Élysées ku Paris ukuŵala kwambiri atayatsa magolobo oposa 100,000 omwe amaikidwa m’mitengo yokwana 300 yomwe ili m’mphepete mwa msewu wotchukawo. Choteronso, sitolo ina yaikulu ikusonyeza mtengo waukulu wa Khirisimasi mu msewu wa m’tauni ya Seoul, Korea, ndipo ukuyamba kuŵala usiku m’likulu ladziko limenelo. Posakhalitsa akukongoletsa misewu yake ndi zokongoletsera za Khirisimasi.
Wailesi yakanema, wailesi youlutsa mawu, ndi manyuzipepala amapanga mapologalamu okhudzana ndi Khirisimasi tsiku lililonse. Posonkhezereka ndi zochitika m’nyengo ya Khirisimasi, chikondwerero cha kutha kwa chaka chimadzaza dziko lonselo. Matchalitchi a mu Seoul, omwe chiŵerengero chawo chimadabwitsa alendo ambiri, awakongoletsa mwamsangamsanga. Choncho, Korea ndi mayiko enanso a Kummaŵa ali kalikiliki kukonzekera Khirisimasi cha panthaŵi imene dziko la United States nalo lili ndi tchuthi chotchedwa Tsiku Lothokoza (Thanksgiving Day) phwando lomwe limachitika kumapeto kwa November.
Mayiko ambiri a Kummaŵa salingaliridwa kukhala m’Gawo la Matchalitchi a Akristu. Mwachitsanzo, 26.3 peresenti yokha ya anthu onse okhala mu Korea ndiwo amati ndi Akristu. Mu Hong Kong ndi 7.9 peresenti, mu Taiwan 7.4 peresenti, ndipo mu Japan ndi 1.2 peresenti yokha basi. Mwachionekere, anthu ambiri a Kummaŵa si Akristu, koma iwo akuoneka kuti alibe choletsa chilichonse ponena za kukondwerera Khirisimasi. Ndithudi, kaŵirikaŵiri iwo amaoneka kukhala achidwi kwambiri ndi Khirisimasi kuposanso anzawo a Kumadzulo. Mwachitsanzo, Hong Kong, ndi dziko lodziŵika kwambiri chifukwa cha mapwando ake adzaoneni a Khirisimasi, ngakhale kuti anthu ambiri a m’dzikolo ndi Abuda komanso Atao. Ngakhalenso ku China, komwe 0.1 peresenti yokha ya anthu kumeneko amadzitcha Akristu, Khirisimasi ikufala mofulumira kwambiri.
N’chifukwa chiyani kukondwerera Khirisimasi kwafala chomwechi Kummaŵa? N’chifukwa chiyani anthu omwe savomereza Yesu kukhala Mesiya amachita nawo Khirisimasi, yomwe ambiri odzinenera kukhala Akristu amati ndilo tsiku lomwe iye anabadwa? Kodi Akristu oona ayenera kutengera malingaliro awo a Khirisimasiwo? Tidzapeza mayankho pamene tidzakambirana mmene Khirisimasi inatchukira m’Korea, dziko lakalekale la Kummaŵa.