Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/15 tsamba 32
  • “Kulimba Mtima Kosonkhezeredwa ndi Chikhulupiriro”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kulimba Mtima Kosonkhezeredwa ndi Chikhulupiriro”
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/15 tsamba 32

“Kulimba Mtima Kosonkhezeredwa ndi Chikhulupiriro”

M’CHAKA cha 1998, panatuluka buku latsopano m’Chifalansa limene linathokozedwa kwambiri ndi akatswiri, lokhala ndi mutu wakuti Les Témoins de Jéhovah face à Hitler (Mboni za Yehova Pamaso pa Hitler), lolembedwa ndi Guy Canonici. M’mawu oyamba a bukulo, wolemba mbiri wachifalansa wolemekezeka kwambiri, François Bédarida analemba kuti: “Ili ndi buku lofunika kwambiri. Osati chabe chifukwa chakuti laulula zobisika, komanso chifukwa chakuti latuluka panthaŵi yake. . . . Kupatulapo akatswiri, ndaninso wina amene akudziŵa za mazunzo omwe Mboni za Yehova zinakumana nawo mu ulamuliro wa Nazi? Komabe, mu ulamuliro wonse wa zaka 12, anakhala akuzunzidwa ngati zinyama ndi ziwawa zosaneneka. Anazunzidwanso m’misasa ya zibalo. Nawonso anapereka nsembe yamtengo wapatali kwambiri kaamba ka chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chiyani olemba mbiri yakale aiwala Akristu amenewa? . . .

“N’chifukwa chiyani ankazunza mwankhalwe chomwecho kagulu kachipembedzo kakang’ono, komwazikana, ndi kosaopsa ngati kameneka? Apa ndiye pagona nkhani. Mboni zinalidi kagulu kakang’ono poyerekeza ndi chiŵerengero cha anthu onse m’Germany​—ziŵerengero zimaonetsa kuti iwo anangokwana 20,000 pa anthu oposa 60 miliyoni​—komanso iwo anali nzika zamtendere omwe ankaopa malamulo ndipo sanawopseze munthu aliyense, koma amangofuna kugwira ntchito ndi kulera bwino ana awo. . . .

“Chizunzo chimenechi chinakumana ndi nyonga yauzimu ya chipiriro chosagonja cha anthu okhulupirira amene anakhoza kuthana ndi mphamvu zakunja mwa chikhulupiriro chawo mwa Yesu Kristu, kuyambira pa chiwawa cha apolisi mpaka pa kupambana kapena kufera chikhulupiriro.”

Nkhani ya Mboni za Yehova zomwe zinalola kufera chikhulupiriro chawo chachikristu, pamaso pa anthu odana ndi chipembedzo n’njamphamvu zedi. Pofotokozanso za bukulo, nyuzipepala yotchuka zedi ya Akatolika ku France, ya Lax Croix inanena mogwira mtima kuti: “Kuchokera m’mbiri yawo yochepayo, Guy Canonici wasonkhanitsa umboni weniweni womwe ungapangitse munthu kukhala kakasi atati amve za kulimba mtima kosonkhezeredwa ndi chikhulupiriro kumene kwanenedwa m’mawu achidule kuti, chikhulupiriro chomwe sichinasweke kufikira mapeto, ngakhale mwa ana. Nkhani yokumbutsa zakaleyi iyenera kupereka chithunzi chenicheni cha mkhalidwe wa Mboni za Yehova pa mkangano womwe ulipo ponena za ukristu wawo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena