Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/1 tsamba 32
  • Kuteteza Dzina Labwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuteteza Dzina Labwino
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/1 tsamba 32

Kuteteza Dzina Labwino

KUYANG’ANA mwachidwi chithunzi chokongola chojambulidwa ndi mmisiri kungakhale kosangalatsa. Titayang’anitsitsa, tingaone mmene mmisiriyo anagwiritsira ntchito bulasho yake kambirimbiri popaka utoto wosiyanasiyana pa nsalu.

Mofananamo, munthu amapanga dzina labwino osati ndi mkwasa umodzi waukulu wa utoto, kunena kwake titero, koma ndi zochita zake zazing’onozing’ono zambirimbiri kwanthaŵi yaitali. Inde, pang’onopang’ono mbiri yathu imakulakulabe molingana ndi zomwe tikuchita.

Komabe, kupaka molakwa mkwasa umodzi wa utoto kungawononge kukongola kwa chithunzicho. Chimodzimodzinso dzina lathu. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake.” (Miyambo 19:3) Utsiru pang’ono​—chiwawa, kumwa moŵa mwauchidakwa, kapenanso kuchita chiwerewere kamodzi basi​—umaipitsa mbiri yabwino ya munthu. (Miyambo 6:32; 14:17; 20:1) Choncho n’kofunika kwambiri kuti aliyense wa ife ayesetse kukhala ndi dzina labwino nalimbikire kuliteteza.​—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena