Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 3/1 tsamba 32
  • Dzina la Mulungu Libwezeretsedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzina la Mulungu Libwezeretsedwa
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 3/1 tsamba 32

Dzina la Mulungu Libwezeretsedwa

“KWA zaka zambiri kapena mazana dzina la Yehova litachotsedwa m’mabaibulo, mboni zake zamakono n’chipembedzo chokha cha Akristu chimene chachirikiza tetragramatonia ndi kuibwezeretsa.”

Mawu apamwambawa atengedwa m’buku lotchedwa Jeová dentro do Judaísmo e do cristianismo (Yehova m’Chiyuda ndi m’Chikristu), lolembedwa ndi Assis Brasil wa ku Brazil. Koma funso lingakhalepo lakuti, Ngakhale kuti matembenuzidwe a mabaibulo ena amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, n’chifukwa chiyani zipembedzo zina zalichotsa m’mabaibulo awo? “Dzina la Mulungu linachotsedwa,” akutero Brasil, “mwina chifukwa cha mwambo . . . , zolinga zobisika, kapena chifukwa chofuna kukweza mayina a Yesu ndi amayi ake, Mariya.”

Komabe, malinga ndi kufotokoza kwa a Brasil: “Mmene munachotsedwa dzina la [Mulungu] mwakonzedwa bwinobwino m’Chipwitikizi ndi New World Translation of the Holy Scriptures.” Motani? Mwanjira yakuti m’Baibulo limeneli dzina la Yehova labwezeretsedwa m’malo ake. Mu New World Translation dzina la Yehova limapezeka kupitirira nthaŵi 7,200.

Kuyambira pamene linatulutsidwa koyamba, Baibulo la m’Chipwitikizi lamakono, komanso lotembenuzidwa motsata liwu ndi liwu limeneli lafalitsidwa mamiliyoni oposa sikisi ndi theka. Chifukwa cha chimenechi, wolemba nkhani m’nyuzipepala ya Diário do Nordeste (Northeastern Daily) ku Brazil anafunsa kuti, “Kodi mumadziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina?” Chifukwa cha matembenuzidwe a Baibulo amakonowa, tsopano anthu mamiliyoni angayankhe kuti, “Inde. Dzina la Mulungu ndi Yehova.”

[Mawu a M’munsi]

a M’chinenero cha Chihebri, dzina la Mulungu limalembedwa motere יהוה. Malembo anayiwa (oŵerengedwa kuchokera kumanja kumka kumanzere) amatchedwa Tetragramatoni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena