Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 32
  • “Phunzitsa Mwana”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Phunzitsa Mwana”
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 32

“Phunzitsa Mwana”

ULIMI wabwino sumangothera pa kumwaza mbewu kokha ndiye kenako n’kudzabweranso patatha miyezi ingapo kudzakolola. Kusosa, kudzala mbewuzo, ndi kuthirira ndi kumazisamalira kuti zizikula kufikira zitakhwima, ndi ntchito yolimba.

Ndondomeko imeneyi ingamveketse bwino choonadi cha Miyambo 22:6, imene imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Indedi, kuphunzitsa kwa makolo ndi kofunika kwambiri pakaleredwe kabwino ka ana.

Komabe, m’dziko lolekererali lerolino, makolo ambiri satsatira uphungu umenewu. Pamene atsatira nzeru yofala yoti ana ayenera kuphunzira kuthana ndi mavuto mwa okha, ana awo nthaŵi zambiri amasiyidwa kuti adzionere okha. Chifukwa cha mchitidwe umenewu, ana amakhala osatetezeka moti angasokonezedwe mosavuta ndi anthu opanda khalidwe ndi opulukira.​—Miyambo 13:20.

Zimakhaladi bwino pamene makolo akhomereza malamulo achikristu mwa ana awo powaphunzitsa za Mulungu adakali aang’ono! Ali aang’ono bwanji? “Kuyambira ukhanda,” akutero mtumwi Paulo. Zinali choncho ndi wachinyamatayo Timoteo. Amayi ake, Yunike, ndi agogo ake aakazi Loisi anamuphunzitsa mwakhama “malembo opatulika” Timoteo kotero kuti ‘anaphunzira’ ndipo ‘anatsimikiza mtima nazo.’ Zotsatira zake? Maphunziro amenewo anamuchititsa kukhala ‘wanzeru kufikira chipulumutso.’​—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

Mofananamo lerolino, makolo amene ‘samalema pakuchita zabwino’ adzatuta mphoto zochuluka ngati ‘akapanda kufooka.’ (Agalatiya 6:9) Mfumu Solomo yanzeru ikuti: “Atate wa wolungama adzasekeradi.”​—Miyambo 23:24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena