Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 10/1 tsamba 32
  • Zikwangwani Mumsewu wa ku Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zikwangwani Mumsewu wa ku Moyo
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 10/1 tsamba 32

Zikwangwani Mumsewu wa ku Moyo

TINENE kuti mukuyenda pamsewu kapena m’kanjira kachilendo, kodi zikwangwani mungamazione ngati zosokoneza ulendo? Iyayi! Ndithudi mungazione kuti nzokuthandizani kukhalabe panjira yopita kumene mukupita.

Nangano bwanji za kuyenda pamsewu wopita ku moyo? Kodi mungautsatire bwinobwino popanda zikwangwani? Mneneri wina wakale wa Mulungu anavomereza kuti munthu sangakwanitse. Iye anati: “Ndikudziŵa, AMBUYE, kuti njira za munthu si zodzisankhira yekha; ndiponso si kwa munthu kusankha njira yake pamoyo.”​—Yeremiya 10:23, The New English Bible.

Tsono chitsogozo chabwinocho chingapezeke kuti? Mlengi wa munthu ndiye angapereke chitsogozo chodalirika chimenecho, ndipo zikwangwani zophiphiritsa zimapezeka m’Baibulo. Mwa Mawu ake, Yehova akuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.”​—Yesaya 30:21.

Inde, Mawu a Mulungu amapereka chitsogozo chodalirika pazochitika zonse za moyo wathu. (Yesaya 48:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Komabe, nzomvetsa chisoni kuti ochuluka mwa mtundu wa anthu akuyenda m’njira ya ku moyo popanda chitsogozo cha Mulungu. (Mateyu 7:13) Komabe, zikwangwani nzozikika pamalo ake! Kodi mudzazitsatira pamene mukuyenda panjira ya ku moyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena