Baibulo Latsopano m’Chigiriki Chamakono
AUGUST 23, 1997, linali tsiku lapadera kwa anthu amene anakapezeka pa Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” ku Greece. Pamapeto a programu yamasana, anatulutsa Baibulo latsopano—New World Translation of the Holy Scriptures m’Chigiriki chamakono. Omvetsera odabwitsidwawo anagwetsa misozi yachimwemwe ndipo anaomba m’manja kwanthaŵi yaitali!
Chiyambire mu 1905, Mboni za Yehova zinkagwiritsira ntchito Baibulo la m’zaka za zana la 19 lomwe linakonzedwa ndi mtsogoleri wachipembedzo cha Greek Orthodox. Baibulo limenelo linawathandiza kwazaka zambiri. Komabe, Mboni za Yehova zinafunitsitsa Baibulo lolondola ndiponso losavuta kumva. Mu 1993, iwo anasangalala pamene analandira Baibulo lachigiriki la New World Translation of the Christian Greek Scriptures (la Malemba Achigiriki Achikristu). Komabe, pamsonkhanowu anasangalala kwambiri pamene Baibulo lathunthu la m’Chigiriki chamakono linatulutsidwa.
Mboni ina poyamikira inatcha New World Translation kuti ndi “ndakatulo, mphepo yayeziyezi yonyamula mawu a Yehova, amene kwanthaŵi yoyamba, tingawamvetsetse m’chinenero chathuchathu.” Ena anayamba kuŵerenga mabaibulo awo atsopano atangofika kunyumba. Winanso amene anakapezeka pamsonkhanowo anaŵerenga Baibulo lake mosangalala mpaka 1 koloko m’maŵa, atamaliza kuŵerenga buku lonse la Yobu!
Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures m’Chigiriki analitembenuza pazaka zisanu ndi ziŵiri za ntchito yolimba. Kalata ina yomwe inalandiridwa inati: “Tingatsimikize kuti Baibulo la New World Translation lidzatithandiza kwambiri pothandiza anthu oona mtima kuti aphunzire za Yehova.”