“Gwiritsitsani Chimene Muli Nacho”
Gulu la Mboni linali kulalikira pa chimodzi mwa zisumbu 30 zomwe zimapanga Zisumbu za Cyclades ku Greece. Pamene Mboni ziŵiri zinali kulalikira m’nyumba za m’mbali mwamsewu, zinakumana ndi wapolisi amene anawatengera kupolisi. Atangofika kupolisiko, telefoni inalira. Wansembe wa m’mudzimo ndiye anaimba telefoniyo. “Ndamva kuti mwafika Mboni za Yehova m’mudzi muno,” iye anatero. “Inde, ndili ndi aŵiri kuno,” anayankha motero wapolisiyo. “Ndibwera posachedwapa.” Malinga ndi mmene anthu aŵiriwo anali kukambitsirana, abale anada nkhaŵa.
Komabe, wansembeyo atafika anamwetulira, anagwirana nawo chanza, nakhala pampando pafupi ndi wapolisi uja. Pamene anapitiriza kukambitsirana, wapolisiyo anayamba kukalipa koma wansembeyo anali wodekha ndiponso waulemu. Anauza wapolisiyo kuti asanyoze Mbonizo, ndipo anawonjezera kuti: “Iwo angayankhe funso lililonse chifukwa chakuti amaphunzitsidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Kungakhale kosavuta kugwedeza dziko lapansi koma nkovuta kufooketsa chikhulupiriro cha mmodzi wa Mboni za Yehova.”
Pamene anali kulalikira m’maŵa mwake, abalewo anakumananso ndi wansembe uja ndipo anamfunsa kuti: “Kodi nchifukwa ninji munatinenera zabwino pamakambitsirano athu kupolisi kuja?” Wansembeyo anawauza kuti anali kugwirizana ndi Mboni zambiri ku Syros ndipo anaŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwazaka zambiri. Kwenikweni, nthaŵi zina amabisa magazini ya Nsanja ya Olonda m’faelo yake nakaigwiritsira ntchito polalikira m’tchalitchi. Iye anati: “Ndiganiza kuti ndikanavutika kwambiri chikhala palibe zofalitsa zanu. Zofalitsa zimenezi ndizo zimandipatsa chiyembekezo.”
Kenaka wansembeyo anauza Mbonizo kuti: “Ndifuna kukuuzani chinthu chimodzi. Gwiritsitsani chimene muli nacho. Musayese kuchisiya. Zimene ndikukuuzanizi ndiwo ulaliki woposa maulaliki onse amene ndaperekapo, ndipo si nthabwala; ndikulankhula kuchokera pansi pa mtima.”