Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/15 tsamba 11
  • “Baibulo la Chala Chimodzi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Baibulo la Chala Chimodzi”
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Chochitika Chosaiŵalika kwa Okonda Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Anthu Miyandamiyanda Padziko Lonse Akuyamikira Baibulo la New World Translation
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Yehova Amalankhula Nafe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • New World Translation
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/15 tsamba 11

“Baibulo la Chala Chimodzi”

ATAPUWALA ndi stroko ya dzuŵa, Joseph Schereschewsky ankalemba kokha patayipi ndi chala chimodzi. Komabe iye anakwaniritsa cholinga chake​—kutembenuzira Baibulo m’chinenero chachitchaina, chimodzi cha zinenero zovuta kwambiri kwa munthu wachilendo.

Schereschewsky, yemwe anali Myuda, atakula anafufuza ndi kuloŵa Chikristu. Kenako anadzakhala mmishonale ku China. Kumeneko, anatembenuza nawo mabuku ambiri, kungoyambira mu 1866 mpakana m’zaka zoyambirira za zana la 20. Popeza kuti anali Myuda, Schereschewsky anali wozoloŵerana kwambiri ndi Chihebri kuposa ophunzira anzake. Pachifukwachi, kutembenuzidwa kwa Malemba onse Achihebri kunaikiziridwa m’manja ake. Chakumapeto kwa ntchito yake ya nthaŵi yaitaliyo, iye anatembenuzanso Baibulo lathunthu lokhala ndi malifalensi m’chinenero chachitchaina.

Monga wotembenuza Baibulo, Joseph Schereschewsky anali wofunitsitsa kuti pakhale matembenuzidwe a Baibulo m’chinenero cha anthu onse. Koma ntchito yake siinali yapafupi. Kutembenuza kwake Baibulo lachitchaina nkochititsa chidwi “chifukwa linali ndi zinthu zambiri ndipo analaka zopinga zambiri pogwira ntchitoyo,” likutero buku lakuti The Book of a Thousand Tongues.

Manja a Schereschewsky atapuwala, iye anapitirizabe kugwira ntchito yakeyo. Anafunikira kulimbikira kwambiri kuti azilemba patayipi chifukwa manja ake sanali kugwira ntchito bwino lomwe. Motero iye anatcha Baibuloli kuti Baibulo lake la chala chimodzi. Kuti alitulutse mosasamala kanthu za mavuto ake, Schereschewsky anapirira kwa zaka 25. Chifukwa chakuti sanaleke ntchitoyo, iye anathandizira kumveketsa Mawu a Mulungu m’Chitchaina​—chinenero chimene chimalankhulidwa ndi anthu ambiri kuposa chinenero china chilichonse.

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Zithunzi zonse ziŵiri: Chilolezo cha American Bible Society Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena