Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/1 tsamba 29
  • Madokotala, Oweruza, ndi Mboni za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madokotala, Oweruza, ndi Mboni za Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/1 tsamba 29

Madokotala, Oweruza, ndi Mboni za Yehova

KUMBUYOKO m’March 1995, Mboni za Yehova zinachititsa misonkhano iŵiri ku Brazil. Cholinga chake? Kufuna kukhazikitsa mgwirizano pakati pa madokotala ndi oweruza pamene wina wodwala m’chipatala ndi mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo sakuvomera kuikidwa mwazi.​—Machitidwe 15:29.

Mwachisoni, nthaŵi zina madokotala ananyalanyaza zosankha za odwala amene ndi Mboni ndipo anakatenga chilolezo kukhoti pofuna kuti odwalawo aikidwe mwazi mokakamiza. Pazochitika monga zimenezi Mbonizo zinayesetsa kupeza chinjirizo lalamulo monga momwe zingathere. Komabe, iwo analingalira zakuti pakhale mgwirizano m’malo moti pakhale makangano. Choncho, misonkhanoyo inagogomezera kuti pali njira zambiri zimene zingaloŵe m’malo mwa kuika wodwala mwazi weniweniwo ndipo Mboni za Yehova zimavomereza njira zimenezi mofunitsitsa.a

Msonkhano wa bungwe lotchedwa Regional Council of Medicine la ku São Paulo unali utagwirizana kale ndi lingaliro la Mboni. M’January 1995 anagwirizana kuti ngati wodwala sakufuna kulandira chithandizo chimene dokotala akufuna kupereka, iye ali ndi ufulu wokana ndi kusankha dokotala wina.

Tikuthokoza kuti tsopano kuli mazanamazana a madokotala ku Brazil amene akufunitsitsa kupereka chithandizo kwa odwala awo popanda kugwiritsira ntchito mwazi malinga ngati odwalawo apempha zimenezo. Kuyambira pamisonkhano imene inachitika m’March 1995, mgwirizano wa pakati pa madokotala, oweruza, ndi Mboni za Yehova ku Brazil wakhala ukuyenda bwino kwambiri. Mu 1997, magazini ina ya zachipatala ku Brazil yotchedwa Âmbito Hospitalar inafalitsa nkhani imene inagogomezera kuti Mboni za Yehova zili ndi ufulu woonetsetsa kuti zosankha zawo pankhani ya mwazi zikulemekezedwa. Tsopano nzodziŵika bwino, monga momwe anafotokozera mabungwe otchedwa Regional Councils of Medicine (Mabungwe a m’Zigawo a Zamankhwala) a m’maboma a Rio de Janeiro ndi São Paulo, kuti “ntchito ya dokotala yotetezera moyo wa wodwala iyenera kulingana ndi ntchito yake yochirikiza ufulu wakusankha wa wodwalayo.”

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna kudziŵa zambiri, onani brosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena