Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 1/15 tsamba 32
  • Limatamanda Mlengi Wake Mwakachetechete

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limatamanda Mlengi Wake Mwakachetechete
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 1/15 tsamba 32

Limatamanda Mlengi Wake Mwakachetechete

KULOŴA kwa dzuŵa kumakhala kokongola mwachilengedwe. Koma kaonekedwe ka dzuŵa likamaloŵa makamaka kuseri kwa phiri limeneli m’mapiri a Apuan Alps ku Tuscany, Italy, nkapaderadi.

Utakhala patali, dzuŵa limaoneka ngati kuti likuloŵa m’phiri limeneli m’malo mooneka kuti likutsikira kuseri kwake. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti nsonga ya phiri limeneli ili ndi pakamwa poyasama mwachilengedwe pamene pamaoneka ngati kuti anachita kupasema. Ndithudi, nsonga imeneyi ndiko kunachokera dzina lake, Monte Forato​—Phiri Lopyozedwa. Popeza kuti dziko limazungulira dzuŵa, awo amene amaona kamwa lotsegukalo, amaona dzuŵa limene limaoneka ngati kuti likuloŵa mkamwa mwa Monte Forato limeneli kaŵiri kokha chaka chilichonse.

Monga zinthu zina zachilengedwe, thambo la zinthu zopanda moyoli limatamanda Mlengi wake. Motani? Monga momwe chithunzi chokongola chimadzetsera chitamando kwa katswiri amene anachijambula. Kwenikweni, zinthu zakuthambo zimalankhula za mphamvu, nzeru, ndi ulemerero wa Yehova. Monga momwe wamasalmo ananenera, “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” (Salmo 19:1; 69:34) Popeza kuti dzuŵa ndi zinthu zina zopanda moyo zimatamanda Mlengi wawo, ndiye kuti ifeyo tiyenera kumtamanda koposa!​—Salmo 148:1, 3, 12, 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena