Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/1 tsamba 32
  • Malamulo Khumi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malamulo Khumi
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/1 tsamba 32

Malamulo Khumi

BISHOPU wina wa ku England, ku Gloucester, anapeza kuti mwa atsogoleri achipembedzo a m’dera lake, oposa theka sankadziŵa kubwereza Malamulo Khumi, ndipo 10 peresenti a iwo sankadziŵa pamene angawapeze m’Baibulo. Koma limenelo linali kale, zaka 450 zapitazo. Kodi zinthu zakhala bwinoko kuyambira pamenepo? Kutalitali​—malinga ndi mmene magazini ya Sunday Times inafufuzira posachedwapa za atsogoleri achipembedzo a Anglican m’madera osiyanasiyana.

Mwa atsogoleri achipembedzo 200 omwe anafunsidwa, 34 peresenti okha ndiwo anatha kutchula Malamulo Khumi onse. Mwa enawo, mmodzi anaganiza kuti malamulowo anali oletsa zinthu zambiri, ndipo wina anangonena kuti ngosathandiza pamavuto amakonoŵa.

Kodi inuyo mumawadziŵa Malamulo Khumi kapena pamene mungawapeze? Alembedwa mu Eksodo, buku lachiŵiri la Baibulo, m’mavesi 17 oyambirira a chaputala 20. Bwanji osawaŵerenga? Nayi njira yapafupi yowaikira m’magulu. Anayi oyambirira amanena za kulambira kwathu Mulungu, lachisanu likunena za moyo wabanja, lachisanu ndi chimodzi mpaka lachisanu ndi chinayi amakhudza unansi wathu ndi anthu anzathu, ndipo lakhumi nlapadera, limatipangitsa kusanthula mitima yathu, kudzipenda. Nayi njira yachidule imene Akristu angagwiritsire ntchito mapulinsipulo ameneŵa.

Loyamba: Tikonde Mlengi wathu ndi chikondi chosagaŵanika. Lachiŵiri: Musagwiritsire ntchito mafano polambira. Lachitatu: Nthaŵi zonse lemekezani ndi kukweza dzina la Mulungu. Lachinayi: Pezani nthaŵi yosumika maganizo pazinthu zauzimu, popanda kudodometsedwa. Lachisanu: Ananu, lemekezani makolo anu. Lachisanu ndi chimodzi: Musaphe. Lachisanu ndi chiŵiri: Peŵani chigololo. Lachisanu ndi chitatu: Musabe. Lachisanu ndi chinayi: Lankhulani zoona. Lakhumi: Peŵani kusirira.

Malamulo Khumi anali ena a malamulo amene Mose anapatsidwa. Koma mapulinsipulo ake amagwira ntchito nthaŵi zonse. (Aroma 6:14; Akolose 2:13, 14) Nchifukwa chake otsatira a Yesu anali kugwira mawu pa Malamulo Khumi pophunzitsa. (Aroma 13:8-10) Moyo ukanakhala wosangalatsa​—ndi wotetezereka chotani nanga anthu onse akanalemekeza mapulinsipulo ameneŵa ouziridwa ndi Mulungu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena