Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/1 tsamba 9
  • Achinyamata Alemekeza Mulungu ku Democratic Republic of Congo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata Alemekeza Mulungu ku Democratic Republic of Congo
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Wodala Ndiwopeza Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/1 tsamba 9

Olengeza Ufumu Akusimba

Achinyamata Alemekeza Mulungu ku Democratic Republic of Congo

ZAKA mazana ambiri kalelo, wamasalmo mwachisangalalo anaitana achinyamata kuti nawonso alemekeze Mfumu yamuyaya: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka.” (Salmo 148:12, 13) Zokumana nazo zotsatirazi za ku Democratic Republic of Congo zikusonyeza mwaŵi wamtengo wapatali umenewu.

• Mwini nyumba yokhalamo mpainiya wina wapadera anakondwera kwambiri ndi khalidwe la Mboni za Yehova. Choncho analola Mboni kuti ziphunzitse Baibulo mwana wake wamkazi wazaka zisanu, Fifi. Ataona kupita patsogolo kwa Fifi pophunzira Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo,a atate wake anamlola kupita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Kumeneko, Fifi wamng’onoyo anaphunzira nyimbo za Ufumu za m’buku la nyimbo la Mboni. Anakonda kwambiri nyimbo nambala 4, yamutu wakuti “Lonjezo la Mulungu la Paradaiso.”

Tsiku lina atate a Fifi anaganiza zopita naye kutchalitchi kwawo. Modabwitsa aliyense, Fifi anakana kuimba nyimbo za tchalitchi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anaona kuti nyimbo zoimbidwa kutchalitchi cha atate ake sizinagwirizane ndi zimene anaphunzira paphunziro lake la Baibulo. M’malo mwake, molimba mtima anaimba nyimbo yake ya Ufumu yapamtima.

Atalephera kumsinthitsa malingaliro ake, atsogoleri a tchalitchi anamchotsa Fifi wazaka zisanuyo! Mosasamala kanthu za kupanda chifundoko, atate ake analeza mtima. Iwo anakondwera kuti Fifi anachirimika pachikhulupiriro chake. Onse aŵiri atate ndi amayi a Fifi akufuna kuti iye apitirize kuyanjana ndi Mboni za Yehova.

• Pamene mnyamata wazaka zosakwanira 20 wotchedwa kuti Lukodi anasankha kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, atate wake sanagwirizane nazo mpang’ono pomwe. Nthaŵi ina pamene Lukodi anali kukonzekera kupita kumsonkhano ku Nyumba ya Ufumu, atate wake anamuopseza ndi chikwanje. Nthaŵi inanso atate a Lukodi anammenya ndi ndodo, kumpanga bala lalikulu kumsana kwake. Mosasamala kanthu za chitsutso chachikuluchi, Lukodi anachirimika pachosankha chake chokhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anapitabe patsogolo ndi kubatizidwa. Tsopano akutumikira monga mpainiya wokhazikika.

Sona, mlongo wamng’ono wa Lukodi, anachita chidwi kwambiri ndi malingaliro a mlongo wake kwakuti iyenso anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe, kuti amletse kuphunzira, atate wawo anatumiza Sona kusukulu ya kumudzi wina, kumene kunalibe Mboni. Komabe, kulankhula kwa ena ponena za zomwe anaphunzira kunakhala chizoloŵezi cha Sona. Chotero, mlongo wake nayenso anachita chidwi.

Pamene Mboni m’mudzi wina wapafupi zinamva za kulalikira kwa Sona, iwo anamchezera ndi kulinganiza kuti akhale ndi phunziro la Baibulo lapanyumba lokhazikika. Iye anapitirizabe kupita patsogolo ndipo posapita nthaŵi anagwirizana ndi mlongo wake monga Mboni ya Yehova yodzipatulira ndi yobatizidwa. Ndiponso, mlongo wake tsopano ali wofalitsa wosabatizidwa, ndipo anayamba kuchita phunziro la buku m’mudzi umenewu.

Nkosangalatsa ndiponso kotsitsimutsa chotani nanga pamene achinyamata nawonso alemekeza dzina la Yehova!

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena