Masiku Osoŵa Tulo Amene Anali Opindulitsa
NGAKHALE mafumu amakhala ndi masiku osoŵa tulo. Wolamulira wamphamvu kwambiri wa Perisiya wa m’zaka za zana lachisanu B.C.E., Ahaswero, anayang’anizanapo ndi zimenezi. Mwinamwake polingalira kuti ananyalanyaza ntchito ina, iye anapempha kuti amuŵerengere buku la mbiri za mafumu. Iye anapeza kuti mtumiki wake wokhulupirika, Moredekai, anaulula za achiŵembu amene anafuna kupha mfumuyo koma sanapatsidwe mphotho iliyonse. Ahaswero anaganiza zothetsa cholakwa chimenechi mwamsanga. Zotsatirapo zopindulitsa za zimene iye anachita kwa anthu a Mulungu zimasonyeza kuti Mulungu ndiye anachititsa kuti mfumuyo isoŵe tulo.—Estere 6:1-10.
Mpingo wa Mboni za Yehova za m’tauni ya Hermanus ya m’mphepete mwa nyanja ku South Africa, unayang’anizana ndi zochitika zimene zimawakumbutsa bwino nkhani imeneyi ya m’Baibulo. Iwo anali kugwiritsira ntchito nyumba ya lendi kaamba ka misonkhano yawo. Iwo anayesetsa kwa zaka zambiri kuti agule malo omangapo Nyumba ya Ufumu yawoyawo. Pomaliza, mu 1991, Konsolo ya Tauniyo inafuna kuwagulitsa malo abwino kwambiri oti amangepo nyumbayo.
Komabe, ena analetsa kuti malo amenewo asagulitsidwe kwa Mboni za Yehova. Nkhaniyi itaimitsidwa kwa miyezi ingapo, mpingowo unauzidwa kuti boma linalamula kuti malo asagulitsidwe kwa matchalitchi mpaka patapita zaka zitatu, choncho mwaŵi wakuti angagule malowo unawathera. M’May 1993, mpingowo unalemberanso konsoloyo ndi kuifunsa kuti ilingalireponso za nkhani imeneyi. Iwo analandira kalata yowayankha yokhala ndi chiganizo chimodzi basi, yonena kuti nthaŵi yoyembekezera inali isanathebe.
Mu October chaka chomwecho, mmodzi wa makansala a m’tauniyo anasoŵa tulo. Posoŵa chochita iye anayamba kuŵerenga nkhani za konsolo pofuna kupeza ngati panali nkhani zina zofuna kuzisamalira. Iye anachita chidwi ndi kalata imene Mboni zinalembera konsoloyo yopempha kuti ilingalireponso za nkhaniyi. Choncho anaganiza zophatikiza nkhani imeneyi pazokambirana pamsonkhano wotsatira. Iye anafuna kukauza osonkhanawo kuti Mboni za Yehova zinafuna kugula malo lamulo loletsa kugulitsa malo kwa matchalitchi lisanakhazikitsidwe.
Kenaka, mpingowo unauzidwa kuti ugule malo amene anawalozera kumbuyoko mu 1991! Malowo ali m’mphepete mwa msewu waukulu, kotero kuti a mumpingomo ndi okondwerera savutika kufikapo. Iwo anamanga Nyumba ya Ufumu yokongola, imene inapatuliridwa kwa Yehova pa October 5, 1996.
Ngakhale kuti mpingowo umavutika maganizo chifukwa cha kusoŵa tulo kwa kansalayo, iye angapeze chitonthozo mwa kulingalira kuti ngakhale Mfumu Ahaswero anasoŵaponso tulo. Ndipo zotsatirapo zake m’nkhani zonse ziŵirizo zinali zopindulitsa. Mpingo wa ku Hermanus ngwoyamikadi kwambiri chifukwa chokhala ndi Nyumba ya Ufumu yawoyawo, malo a kulambira koyera ndi maphunziro a teokrase m’tauni yodziŵika bwino imeneyi ya m’mphepete mwa nyanja.—Ahebri 10:24, 25.