Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/1 tsamba 3
  • Nthaŵi Zovuta kwa Okalamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Zovuta kwa Okalamba
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kusamalira Okalamba—Vuto Lomakulakulabe
    Galamukani!—1991
  • Kukwaniritsa Zosowa za Okalamba Athu—Chitokoso cha Mkristu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/1 tsamba 3

Nthaŵi Zovuta kwa Okalamba

MAYI ONIYAN, amene ali ndi zaka 68, amakhala mumzinda waukulu wa ku West Africa. Pamene anali wamng’ono, ankaganiza kuti adzasangalala m’zaka zake zaukalamba pa penshoni yake mosatekeseka konse, atazingidwa ndi ana ndi adzukulu ake. M’malo mwake nthaŵi zonse amagulitsa madzi ozizira padzuŵa lotentha la mu tropic. Iye amathandizidwa ndi ndalama zochepa zimene amapezazo. Ana ake aŵiri aamuna amakhala m’dziko lina lakutali. Papita nthaŵi yaitali kuchokera pamene anamtumizirapo ndalama.

Nthaŵi zakale, okalamba a ku Afirika ankalemekezedwa kwambiri. Ankalemekezedwa chifukwa cha luso ndi chidziŵitso chawo, pamodzi ndi nzeru ndi kuzindikira zimene ameneŵa amapatsa nthaŵi zambiri. Ankathandizira kulera adzukulu. Achinyamata anali kufunafuna malangizo ndi chiyanjo chawo. Anthu ankakhala mogwirizana ndi uphungu wa Baibulo wakuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.”​—Levitiko 19:32.

Nthaŵi zasintha. Umphaŵi, kutsika kwa mphamvu ya ndalama, ulova, ndi kusamuka kwa anthu ambiri kukakhala kumizinda zapangitsa kuti okalamba ambiri azidzipezera zosoŵa movutikira. Mkulu wa bungwe la HelpAge Kenya, Camillus Were, akunena kuti: “Mwambo wothandiza ndi kusamalira okalamba ukufookerafookera.”

Zoonadi, kufooka kwa mgwirizano wa achibale sikuchitika m’maiko a ku Afirika okha. Ponena za ku Japan, Guardian Weekly ikunena kuti: “Kudzipereka kwa ana kunali maziko amakhalidwe abwino achijapani operekedwa ndi chikomfyushanizimu koma kwazimiririka chifukwa chosamukira ku matauni ndi kufooka kwa mgwirizano wa achibale: lerolino, 85 peresenti ya Ajapani amafera m’zipatala kapena m’nyumba zosungiramo anthu okalamba.”

Mulimonse mmene zingakhalire, amene amafunitsitsa kusangalatsa Mulungu amayesetsa kulemekeza makolo awo. Iwo amatsatira uphungu wa Baibulo wakuti: “Lemekeza atate wako ndi amako . . . kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:2, 3) Ngakhale kuti sikukhala kwapafupi nthaŵi zonse kulemekeza ndi kusamalira makolo okalamba, kungabweretse mapindu ochuluka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena