Anaima Nji pa Chizunzo cha Anazi
KUKHULUPIRIKA mosaopa kwa Mboni za Yehova m’Germany wolamulidwa ndi Anazi nkodziŵika bwino poyerekeza ndi zomwe matchalitchi a Dziko Lachikristu amachita. Izi zinanenedwa ndi profesa wa za mbiri yakale John Weiss m’buku lake lakuti Ideology of Death. Iye akulemba kuti:
“Mu 1934 tchalitchi cha Evangelical chinalimbikira kunena kuti Anazi ayenera ‘kulandiridwa ndi a Lutheran,’ ndipo anathokoza ‘Ambuye Mulungu,’ popatsa a Germany ‘mtsogoleri wamphamvu ndi wokhulupirika.’ . . . Bishopu wachiprotestanti analembera abusa m’mipingo kuti, ‘[Hitler] watumizidwa kwa ife ndi Mulungu.’” Weiss akupitiriza kuti: “Tchalitchi cha Methodist cha ku Germany . . . chidagwirizana ndi Bishopu Dibelius kuti Hitler wapulumutsa Germany pa chiopsezo cha gulu lopanduka la Bolshevik ndi kubweretsa mtendere ndi bata . . . Tchalitchi cha Mormon chinalangiza mamembala ake okhulupirika kuti kutsutsana ndi Hitler ndi kuphwanya lamulo la Mormon.” Iye anawonjezera kuti: “Akatolika anauzidwa kuti kumvera boma latsopanolo kunali chinthu chopatulika, ndipo sanaleke kutero ngakhale pamene anadziŵa zoipa zimene Anazi amachita m’maiko akummaŵa.”
Koma bwanji ponena za Mboni za Yehova? Profesa Weiss akunena kuti “Mboni za Yehova zokha, monga gulu, zinatsutsa zochita za Anazi. Zikwi za izo zinaponyedwa m’ndende, profesa Weiss akupitiriza kuti, “komatu Mboni iliyonse imene inatumizidwa ku msasa wa chibalo ikanamasulidwa mwakungosaina pepala kuti yaleka chipembedzo chake.”
Ponena za kukhulupirika kwa Mboni za Yehova, Profesa Weiss akunena kuti: “Chitsanzo chawo chimasonyeza kulimba mtima kwapadera ndi mphamvu zomwe Chikristu choyambirira chinali nazo kulinganizidwa kwake ndi kuyamba kwake kuloŵerera zochita za anthu kusanakhale chopinga pa kusagonjera. Monganso momwe pasitala wachiprotestanti wina analembera za iwo, ‘Si matchalitchi akuluakulu, koma anthu awa onenezedwa ndi onyozeka ndiwo amene anayamba kutsutsa ukali wa chiŵanda cha Anazi, ndipo ndiwo anatha kutsutsa malinga nchikhulupiriro chawo.’”