Mboni za Yehova Zitafika Panyumba Panu
Kodi Akatolika ayenera kuchitanji mmodzi wa Mboni za Yehova atafika panyumba pawo? Chofalitsa chaposachedwa chimene inakonza National Catechistic Bureau of the Italian Bishops’ Conference chinati: “Kukana mwaulemu komanso molimba kuti simufuna kulankhula nawo si kupanda chifundo ayi.”
Malinga ndi zimene inasonyeza kalata imene mwamuna wina wa ku Foggia, Italy, anatumiza ku nyuzipepala ya masiku onse yakuti Gazzetta del Mezzogiorno, si Akatolika onse amene akuvomerezana nazo zimenezo:
“Sindine mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndine Mkatolika. Koma ndadabwa nawo malamulo ena omwe tchalitchi chikuumiriza pa anthu ake, kuwauza kumamatiza mawu pazitseko zawo opitikitsa Mboni za Yehova. Komatu anthu ameneŵa amangonyamula Mawu a Mulungu, ndipo amathandiza ena kudziŵa Baibulo kwambiri. Zikundikumbutsa nthaŵi imene kolera inabuka m’Italy muno ndipo tinapatsidwa uphungu mmene tingaipewere.
“Mmene ndikuonera, zimenezi zikusonyeza kuti tchalitchi chikuumiriza malamulo akeake osaganizako zimene anthu ake akufuna. Koma pazaka zingapo tsopano, ndaona kuti ngakhale Akatolika amapita kunyumba ndi nyumba, kuchezera ngakhale nyumba za Mboni za Yehova; ndipo izo zimawalola, kukambitsirana nawo osakana aliyense.”
Mboni za Yehova sizimakakamiza anthu kulandira uthenga wawo. M’malo mwake, zimayesetsa kuuzako ena za chiyembekezo chomwe Mawu a Mulungu amapatsa chimene chazitonthoza izo nthaŵi zino zovuta. Mwa kupita kunyumba ndi nyumba, ndiponso mwa kulankhula ndi aja omwe zimakumana nawo m’makwalala, Mboni za Yehova zimauzako aja ofuna kumva za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14; Machitidwe 5:42; 17:17.