Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 32
  • Kusenza Goli Ukali Wamng’ono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusenza Goli Ukali Wamng’ono
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 32

Kusenza Goli Ukali Wamng’ono

MU “Nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, achichepere amakumana ndi ziyeso zambiri. (2 Timoteo 3:1) Tsiku lililonse amamva manenanena olimbikitsa chiwerewere, kusuta, ndi makhalidwe ena oipa. Omwe amatsatira miyezo ya Baibulo angasekedwe chifukwa chokana kutsatira zomwe gulu likuchita, ndipo Akristu ena angaone kuti kugonja ndiko kwapafupi.

Chakumapeto kwa zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., Yeremiya analemba kuti: “Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.” (Maliro 3:27) Kodi anatanthauzanji? Anatanthauza kuti kuphunzira kulimbana ndi mavuto ukali wamng’ono kumathandiza kuti udzathe kulimbana ndi mavuto aakulu utakula. Masoka, ngakhale ali osakondweretsa, ngosapeweka kwa Mkristu wachichepere kaya wachikulire. (2 Timoteo 3:12) Koma phindu la kukhulupirika limaposa mpumulo wosakhalitsa womwe kugonja kungabweretse.

Ngati ndinu wachichepere, limbanani ndi ziyeso zachikhulupiriro molimba mtima. Pamene muyesedwa kuti muyambe kuchita choipa, musagonje. Ngakhale kuti pa nthaŵiyo zingakhale zovuta kuchita zimenezi, mudzakhala ndi nkhaŵa zocheperapo. Yesu analonjeza kuti: “Senzani goli langa,. . . ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”​—Mateyu 11:29, 30.

Lolerani mavuto obwera chifukwa chokhala mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Kutero kudzakupatsani njira yabwino ya moyo tsopano ndiponso chiyembekezo chodalirika cha mtsogolo. Monga momwe Baibulo limanenera, “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”​—1 Yohane 2:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena