Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/15 tsamba 32
  • Choonadi Ponena za Helo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Choonadi Ponena za Helo
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/15 tsamba 32

Choonadi Ponena za Helo

LIPOTI la bungwe la Church of England lofufuza chiphunzitso linatero kuti helo si ng’anjo yamoto konse; m’malo mwake, ndi malo omwe kulibe, omwe anthu amangoganizira. “Pali zifukwa zambiri zosinthira chimenechi,” lipotilo linafotokoza choncho. “Koma china nchakuti Akristu ndi akunja omwe posonkhezeredwa ndi chikhalidwe ayamba kutsutsa chipembedzo chowopsa, ndipo ambiri azindikira kuti chithunzi cha Mulungu amene amazunza kwamuyaya anthu mamiliyoni ambiri nchosemphana ndi vumbulutso la chikondi cha Mulungu mwa Kristu.”

Si a Church of England okha omwe ali ndi nkhaŵa chifukwa cha lingaliro limeneli la mwambo ponena za helo. Anthu a zipembedzo zosiyanasiyana kumawavuta kulambira Mulungu wankhanza yemwe amawotcha ochimwa. “Anthu amafuna Mulungu yemwe ndi wachifundo ndi wokondeka,” akutero Jackson Carroll, profesa wa chipembedzo ndi chikhalidwe cha anthu, ku Divinity School, ya pa Yunivesite ya Duke. “Nkosemphana ndi chikhalidwe chalero kulankhula za uchimo ndi liwongo.”

Kwa nthaŵi yaitali Mboni za Yehova zakhulupirira kuti helo, monga mmene Baibulo limaphunzitsira, ndi manda wamba chabe a anthu akufa​—osati malo achizunzo chamoto. Sikuti ali ndi lingaliro limeneli chifukwa chakuti nlofala iyayi, koma chifukwa cha zimene Baibulo limanena: “Koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . , mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda [“helo,” Douay Version yachikatolika].”​—Mlaliki 9:5, 10.

Pozindikira bwino mkhalidwe wa akufa, Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, analemba kalelo mu 1896 kuti: “Sitimapeza [m’Baibulo] malo oterowo achizunzo chamuyaya monga mmene matchalitchi ndi mabuku anyimbo, ndi alaliki ambiri amaphunzitsira molakwa. Koma tapezamo ‘helo,’ sheol, hade, kumene mtundu wathu wonse unaweruzidwirako chifukwa cha tchimo la Adamu, ndipo kumene onse awomboledwako mwa imfa ya Ambuye wathu; ndi kuti ‘helo’ ndi manda​—mkhalidwe wa imfa.”

Chotero kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni za Yehova zakhala zikuphunzitsa choonadi cha Baibulo ponena za helo.

[Chithunzi patsamba 32]

Charles T. Russell

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena