Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 8
  • Kufikitsa Choonadi kwa Osiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufikitsa Choonadi kwa Osiyanasiyana
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi N’zothekadi Kuti Khalidwe la Anzanga Lingandisokoneze?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?
    Galamukani!—2014
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamatengeke N’zochita za Anzanga?
    Galamukani!—2003
  • Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Kufikitsa Choonadi kwa Osiyanasiyana

MTUMWI Paulo anali wolengeza wachangu wa Ufumu wa Mulungu. Sanalole chitsutso kumletsa ntchito yake yolalikira “uthenga wabwino.” (1 Akorinto 9:16; Machitidwe 13:50-52) Paulo analimbikitsa ena kutsatira chitsanzo chake.​—1 Akorinto 11:1.

Mboni za Yehova nzodziŵika padziko lonse chifukwa cha khama lawo lakulalikira. Ndithudi, zimalankhula ndi ena ponse paŵiri “panthaŵi yake” ndi “popanda nthaŵi yake” kuti akwaniritse ntchito yopatsidwa ndi Mulungu ya ‘kupanga ophunzira.’ (2 Timoteo 4:2; Mateyu 28:19, 20, NW) Ngakhale m’maiko mmene amakumana ndi chitsutso, anthu oona mtima akufikiridwa ndi uthenga wofunika umenewu wonena za Ufumu wa Mulungu, monga momwe zokumana nazo zotsatirazi zikusonyezera.

◻ Pachisumbu china chakumadzulo kwa Pacific kumene ntchito ya Mboni za Yehova njoletsedwa, mnyamata wina wazaka 12 anapeza kuti mabwenzi ake kusukulu anali oipa. Amkalasi anzake ambiri anali kumasuta ndudu nthaŵi zonse, kuŵerenga mabuku azaumaliseche, kuvutitsa aphunzitsi, ndi kuchita ndewu. Mkhalidwewo unafika poipa kwambiri kwakuti mnyamatayo anapempha atate wake kuti amsinthire kusukulu ina. Komabe, tateyo anakambitsirana ndi mwana wakeyo kuti asasamuke, pakuti anaganiza kuti khalidwe la ana a m’masukulu ena apafupi ndi limodzimodzi. Koma kodi akanamthandiza bwanji mwana wake?

Tateyo anakumbukira kuti anali ndi buku la achichepere m’nyumba. Linali mphatso yochokera kwa wachibale yemwe anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Choncho analifunafuna bukulo, ndipo atalipeza, anampatsa mwanake uja. Linali ndi mutu wakuti: Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza.a Mnyamatayo anapeza mutu wakuti “Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanga?” kukhala wothandiza kwenikweni. Silinangomphunzitsa kufunika kwa kudzisungira ulemu waumwini komanso linamphunzitsa mmene angakanire mwaluso pamene ena anayesa kumuumiriza kutenga njira yopusa. Mwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a m’Malemba, mnyamatayo anaphunzira mmene angalakire chitsenderezo cha mabwenzi.

Ataona masinthidwe abwino ameneŵa ndi enanso mwa mwana wake, tateyo anaganiza zoliŵerenga bukulo. Atachita chidwi ndi uphungu wothandiza wopezeka m’bukulo, tateyo anapempha Mboni za Yehova kuti zimphunzitse Baibulo. Pambuyo pake, ziŵalo zina za banja lake zinayamba kukhalapo paphunzirolo. Chotulukapo chake? Mnyamatayo, mphwake, atate wake, ndi agogo ake aŵiri tsopano ndi Mboni za Yehova.

◻ M’dziko limodzimodzilo, Mboni za Yehova ziŵiri zinaponyedwa m’ndende chifukwa cha kumvera kwawo mosamalitsa mapulinsipulo a Baibulo. Komabe, sanalole mkhalidwewo kuwalepheretsa kulankhula molimba mtima za Ufumu wa Mulungu. Anafikira ofesala wandende ndi kupatsidwa chilolezo kuti achitire komweko chikumbutso cha Mgonero wa Ambuye. Anali okondwa chotani nanga pamene akaidi 14 anakondwera ndi za m’Baibulo ndi kukhala nazo Mbonizo pa chochitika chofunika chimenechi! Atamasulidwa, ena a iwo anapitiriza kuphunzira Baibulo ndi kusonkhana ndi Mboni za Yehova.

M’maiko oposa 25 Mboni za Yehova zikuvutitsidwa chifukwa cha ziletso kapena mitundu yosiyanasiyana ya chitsutso kapena chizunzo. Komabe, mofanana ndi atumwi, zimapitiriza ‘osaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’​—Machitidwe 5:42.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena