Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/15 tsamba 32
  • Kodi Onse ndi Mavumbulutso a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Onse ndi Mavumbulutso a Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/15 tsamba 32

Kodi Onse ndi Mavumbulutso a Mulungu?

KODI mzimu wa Mulungu, umene unauzira Baibulo Loyera, ungakhalenso womwewo umene unauzira mabuku ena omwe ena amawalingalira kukhala oyera? (2 Timoteo 3: 16) Funso limeneli linafunsidwa m’magazini a Ajezuti a ku Italy (La Civiltà Cattolica) ofalitsidwa “moyang’aniridwa ndi bungwe la [Vatican] Secretariat,” chotero olingaliridwa kukhala aukumu m’magulu a Akatolika.

“Mulungu, mogwiritsira ntchito Mzimu Woyera, anamwazira mbewu ya Mawuwo ngakhalenso m’mabuku ena amene sali a mwambo wachiyuda ndi Chikristu,” anatero magazini a Ajezutiwo. Kwa Ajezuti, mabuku “oyera,” onga Zoroastrian Avesta kapena Mabuku Anayi Achikonfyushiani (Confucian Four Books), “sanalembedwe popanda chisonkhezero chinachake cha Mzimu Woyera, chotero, pamlingo waung’ono, ali ndi ‘vumbulutso la Mulungu.’”

Komabe, nkhaniyo ikumveketsa bwino kuti: “Si kuti zonse zimene mabuku oyera oterowo ali nazo ndi mawu a Mulungu,” ikufotokoza choncho, ikumawonjezera kuti awo omwe analemba mabuku amenewo angakhale “atasonkhezeredwa ndi anthu azikhulupiriro zosiyanasiyana pamalo kapena m’dera la zafilosofi” limene anakhalako ndi kuchita zinthu. Malinga ndi kunena kwa Marco Politi, mtolankhani wa nyuzipepala yachitaliyana ya zochitika za ku Vatican La Repubblica, chikhulupiriro chimenechi “chiyambitsanso maunansi amene kumbuyoku sanaganiziridwe kuti angakhale othekera pakati pa Tchalitchi Chakatolika ndi zipembedzo zazikulu za m’mbiri,” kuyambitsanso mzimu wa mapemphero amisonkhano yosiyanasiyana yazikhulupiriro zonse monga uja unali ku Assisi mu 1986, umene unachirikizidwa mwamphamvu ndi John Paul II.

Yehova sali Mulungu wachisokonezo ndi wopanda dongosolo. (1 Akorinto 14:33) Choncho sitingagamule moyenerera kuti mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito, unatha kuuzira ngakhale kachigawo kamabuku alionse amene sali ogwirizana kwenikweni ndi Mawu ake, Baibulo. M’malo mwa kulimbikitsa lingaliro lachigwirizano cha zipembedzo za “miyambo yosiyanasiyana,” mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti pali “chiyembekezo chimodzi . . . , Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.”​—Aefeso 4:4, 5.

“Chiyembekezo chimodzi” chimenecho chimadalira pa kuika chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. Moyenerera Baibulo limati: “Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe. 4:12) Palibe “buku loyera” lina limene limadziŵikitsa Yesu monga munthu wofunika kwambiri pakukwaniritsidwa kwa zifuno za Mulungu. Kokha ngati tililandira Baibulo monga Mawu a Mulungu lingatiphunzitse za makonzedwe achikondi a Yehova Mulungu a chipulumutso.​—Yohane 17:3; 1 Atesalonika 2:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena