Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/15 tsamba 20-21
  • “Ndiye Tchalitchi Chanu Chili Kuti?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndiye Tchalitchi Chanu Chili Kuti?”
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/15 tsamba 20-21

“Ndiye Tchalitchi Chanu Chili Kuti?”

MBONI ZA YEHOVA m’Mozambique kaŵirikaŵiri zimafunsidwa funso limeneli. Mosabisa mawu, limeneli linali funso lovuta kuyankha mpaka dzulodzuloli. Zinali choncho chifukwa chakuti Mboni za Yehova sizinali zovomerezedwa mwa lamulo m’dzikoli kufikira 1991. Chotero, sikunali kotheka kukhala ndi malo odziŵika bwino ndi okhazikika olambirira.

Komabe, mkhalidwe umenewo unasintha pa February 19, 1994. Patsiku ladzuŵa lotentha limenelo, Nyumba za Ufumu ziŵiri zoyamba kumangidwapo m’Mozambique zinapatuliridwa. Anthu okwanira 602 analipo popatulira malo abwino osonkhanira ameneŵa mu mzinda wa doko wa Beira, chapafupifupi ndi gombe la Mozambique. Zidzakwaniritsa zosoŵa za mipingo itatu mu mzindawo.

Ntchito yonse, kuyambira pakumanga maziko mpaka kutsiriza nyumbazo, inali ntchito yamphamvu ya chaka chimodzi ndi miyezi iŵiri. Kaŵirikaŵiri antchito odzifunira 30 kapena oposerapo ochokera ku Zimbabwe chapafupi anali kumabwera ndi kumagwira ntchito mogwirizana ndi Mboni za momwemo. Popeza kuti malo ogona sanawakwanire onsewo m’nyumba ya amishonale m’Beira, imene inatumikira monga malikulu a ntchitoyo, ena anamanga misasa mozungulira nyumbayo kumapeto kwa mlungu ndipo nthaŵi zina kwa milungu ingapo.

Malo a Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Massamba ndi wa Munhava ali m’mbali mwa msewu waukulu wa Beira. “Patsiku lakalikiliki, pamene ntchito inagundika ndipo kupita kwake patsogolo kunayamba kuonekera,” anatero mmishonale wina, “tinali kutsala nenene kuona ngozi pamene oyendetsa magalimoto analikudutsa maso ali dwii pa Nyumba ya Ufumuyo, pafupifupi kuiŵala ziwongolera zawo.” Ambiri anaimadi nkumapenyerera ntchitoyo, ndipo anachita chidwi kwenikweni ndi mafuko osiyanasiyana omwe analipo omagwira ntchito limodzi.

Panali kukonzekera ndi kulinganiza kochuluka pantchitoyo. Mosiyana ndi ntchito zomanga zina ambiri m’mbali ino yadziko, kumene milimo ndi zipangizo zili zovuta kupeza, sizinachitikepo kuti ntchito yomanga Nyumba za Ufumuzo nkuima chifukwa chosoŵa zomangira. Pa nthaŵi ina, matumba 800 a sementi anafunika, ndipo malo amodzi okha kumene akanapezekako kunalibe matumba oyenera oikamo sementiyo. Abale anatumiza uthenga ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu mzinda waukulu, Maputo; matumba anatumizidwa pandege, naperekedwa ku fakitale yasementiyo, nkudzazidwa. Ntchitoyo inapitiriza mosadodometsedwa.

Pa nthaŵi inanso, pamene anali kupachika denga, omangawo anapereŵedwa mitanda yachitsulo. Chifukwa cha kusapezeka, zitsulo za chimangocho zinali zitagudwa kutali pamtunda wa makilomita 600! Wantchito mmodzi anafikira munthu wina yemwe anali kupenyerera ndi kumfunsa ngati anadziŵa kwina kumene iwo akanatha kupeza zitsulo zoti atsirizire ntchito. Munthuyo anayankha kuti: “Ndakhala ndili chilili pano koposa ola limodzi, ndipo sizingakhale zitangochitika mwa malunji. Ndingosiriratu basi ntchito mukugwirayi ndi kudzipereka kwanu pantchitoyi. Ndili nazo zitsulo zimene mukufunikirazo, ndipo ndingakondwe kuzipereka kwa inu monga mphatso.” Chimenechotu ndiye chinangokhala chopereka cha panthaŵi yoyenera.

Openyerera ambiri anali kudabwa kuti ndi kampani yaikulu yomanga iti imene inali kuchirikiza ntchito imeneyi. Ndithudi, omangawo anali kumamva chimwemwe chachikulu pomaŵauza kuti izi zinali Mboni za Yehova zodzipereka kugwira ntchito. Kodi nchiyani kwenikweni chimene chinali kuwachititsa chidwi openyererawo? “Ndinu anthu ogwirizana,” anatero wina. “Ngakhale muli a mafuko osiyanasiyana, mumagwira ntchito limodzi monga abale.” Chotulukapo chake chinali chakuti ambiri anabwera kudzapempha maphunziro a Baibulo. Zinawasonkhezeranso kusonkhana. Mwachitsanzo, avareji ya opezeka pamsonkhano pa mpingo wa Manga inaposa kaŵiri chiŵerengero cha Mboni.

Ndithudi Nyumba za Ufumu zatsopanozo zakhaladi dalitso lalikulu kwa Mboni zakumaloko. Papitapo ambiri anali kusonkhana m’malo osasamalika ofoleledwa ndi udzu kapena malata azitini, kukhonde, kapena m’chipinda chaching’ono cha nyumba ya munthu wina. Kaŵirikaŵiri anali kunyoŵa pamene mvula inavumba; komabe anali kumapezeka pa misonkhano mokhulupirika. Kwa zaka makumi ambiri zimenezi zinali “Nyumba za Ufumu” zokha zimene Mboni za m’Mozambique zinadziŵa. Mbale Caetano Gabriel, mkulu mumpingo wa Massamba, anati: “Tikuthokoza abale athu padziko lonse amene anathandizira kutheketsa ntchito imeneyi.” Mboni ina yachichepere inakumbukira kuti: “Pamene tinali ku Carico (“malo a kuphunzitsidwanso” kumene Mboni za Yehova zinabindikiritsidwa pafupifupi zaka 12), tinali kunena kuti, ‘Tidzapirirabe mokhulupirika, ndipo Yehova adzatifupa.’ Nyumba ya Ufumu yatsopanoyi ndiyo mfupo yochokera kwa Yehova.” Mawu awo amasonyeza chiyamiko chachikulu ndi chitsimikizo chawo cha kutamanda Yehova.

Achichepere ambiri amene anatengamo mbali m’ntchito yomanga anatengeka ndi mzimu waupainiya ndipo pambuyo pake anafunsira utumiki waupainiya wokhazikika. Isabel wachichepere, mpainiya wanthaŵi zonse mumpingo wa Manga, anadzuma pamene anali kuyang’ana Nyumba ya Ufumu yaudongo wadzaoneni ikuyembekezera kupatuliridwa mmaŵa mwake: “Kwa ine ano ndiwo malo okongola kopambana mu mzinda wa Beira. Nkosangalatsa kwambiri kwa ine kukhala pano.” Adão Costa, mmishonale, anafotokoza kuti mafumu apamalopo anali ogwirizanika pololera makonzedwe apadera ogulira katundu kunja chifukwa anadziŵa za kuona mtima kwa Mboni. Ndiyeno anaonjezera kuti: “Ngakhale kuti tinatopa kwambiri, kunali kosangalatsa kuona zipatso za ntchito imeneyi ya ulemu ndi ulemerero wa Yehova.”

Tsopano, paliponse pamene nzika yaubwenzi ya mu mzinda wa Beira ifunsa kuti, “Ndiye tchalitchi chanu chili kuti?” Mbonizo zimamsonyeza imodzi ya Nyumba za Ufumu ziŵiri zatsopanozo ndi kuyankha ndi mawu onga akuti: “Chili mu International Road, Avenida Acordo de Lusaka, moyang’anizana ndi Fourth Squadron Police Station.” Kenako, nkumuongolera pang’ono, “Kokha kuti si tchalitchi. Ndi Nyumba ya Ufumu!”

[Mapu/​Zithunzi patsamba 20]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

Mozambique

Beira

Maputo

[Mawu a Chithunzi]

Mapu: Mountain High Maps® Copyright © 1995 Digital Wisdom, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena