Kuyenera kwa Chivomerezo Chodziŵa Kutsimikizidwanso
CHIWERUZO chaposachedwapa choperekedwa ndi Woweruza wa Zofufuza Zoyamba za Khoti la Messina, ku Italy, chatsimikizanso kuti madokotala ayenera kutsatira machiritso amene wodwala wamsinkhu wasankha. Chiweruzocho chinaperekedwa pa mlandu wokhudza mmodzi wa Mboni za Yehova.
Mu January 1994, Antonino Stellario Lentini Mboni ya zaka 64 yodwala hemophilia, anapititsidwa kuchipatala ku Taormina, Messina. Mkazi wa Antonino, Catena, anauza antchito a m’chipatalamo kuti monga Mboni za Yehova, iyeyo ndi mwamuna wake sangalole machiritso oika mwazi. (Machitidwe 15:20, 28, 29) Zofuna zawo zinalemekezedwa.
Komabe, paulendo womka kuchipatala china, Antonino anayamba kulephera kupuma ndipo anafika ali wodwala kwambiri. Posapita nthaŵi pambuyo pake, anamwalira. Catena anagwidwa ndi chisoni chachikulu, koma anapeza chitonthozo chachikulu pa lonjezo la Baibulo la chiukiriro. (Machitidwe 24:15) Ndiyeno, modabwitsidwa kwambiri, amejastiliti—mwinamwake atasokeretsedwa ndi nyuzi zolakwika zoulutsidwa ndi ofalitsa nkhani—anampatsa mlandu wa kuchititsa imfa ya mwamuna wake chifukwa chakuti anakana machiritso amene madokotala anaona kuti anali ofunika.
Koposa chaka chimodzi pambuyo pake, pa July 11, 1995, Catena anaonjoka, popeza sanachite cholakwa chilichonse. Kwenikweni, umboni wa akatsŵiri unasonyeza kuti, malinga ndi mkhalidwe wa wodwalayo, machiritso alionse sakanagwirabe ntchito.
Koma mawu a woweruza ndiwo anasonyeza nkhani yaikulu. Iye anasonyeza kuti nkovuta kulandira lingaliro lakuti antchito za m’chipatala ayenera kuloŵererapo pamene wodwala kapena anthu omuimira akana machiritso akutiakuti. Anawonjezera kuti lamulo lonena za thayo pa zamankhwala mu Italy “likuoneratu kufunika kwa kukhala ndi chivomerezo chodziŵa cha munthu wokhudzidwa chilichonse chisanachitidwe.” Chotero, ananena kuti Catena “anatetezera mwamuna wake mwalamulo kuti asachitidwe opaleshoni yotero.”
Chiweruzo chimenechi chimatsimikizanso kuyenera kwa wamsinkhu kukana machiritso amene atsutsana ndi zofuna zake.