Anachirikizidwa ndi Bwenzi Lawo Lalikulu Koposa
PALI ubwenzi wina wapadera umene umachilikiza Mboni za Yehova. Ndiwo unansi wamtengo wapatali umene ali nawo ndi Bwenzi lawo lalikulu koposa, Yehova Mulungu. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:23.) Iye amazichirikiza m’nthaŵi ya ziyeso zazikulu za chikhulupiriro chawo.
Mbiri ya umphumphu wa Mboni pansi pa maboma otsendereza yatamandidwa ndi openyerera ambiri. Mmodzi wa iwo ndi Jiří Krupička, katswiri wa filosofi ndi sayansi ya zachilengedwe amene anasamuka kuchokera ku Czechoslovakia mu 1968 atakhala zaka zambiri m’misasa yachibalo ya Komyunizimu. M’buku lake lakuti Renesance rozumu (Kubadwanso kwa Anzeru), akuthirira ndemanga pa kuvutika ndi kusagwedezeka kwa Mboni zimene zinaponyedwa m’ndende kaamba ka uchete wawo.
Pansi pa boma lachikomyunizimu, Mboni zambiri zinaponyedwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti zinali m’ndende, zinakana kukumba m’migodi uranium yogwiritsira ntchito m’zankhondo. (Yesaya 2:4) Krupička akulongosola zimene anaona mu umodzi wa migodi imeneyi mu 1952. Iye anaona anthu aŵiri ataimirira monga zifaniziro zoumba zokutidwa ndi madzi oundana m’chisanu chozizira koposa. Anavundikiridwa kumutu ndi zitini zofika mchuuno.
Krupička akulemba kuti: “Iwo anali ataimirira pamenepo atavala nsanza za m’ndende kuyambira mmaŵa kwambiri. Kodi anakhoza motani kuimirira kwa nthaŵi yaitali motero ndi miyendo youma ndi kuzizira? Mwa mphamvu ya chikhulupiriro. Zitinizo zinali zakale ndi zadzimbiri. Munthu wankhalwe anawamenya pamitu ndi paphewa pawo mwamphamvu kwambiri kwakuti mlomo wowonongeka wa zitinizo unang’amba chovala ndi kucheka khungu la mmodzi wa amunawo, ndipo mwazi unali kuchucha m’malaya ake.
“Mlondayo anaimika gulu lathu patsogolo pawo, ndipo ofesala wamkulu analankhula kwa ife zochititsa kakasi. Iye anati wokana kugwira ntchito ndi mpandu, ndipo ayenera kupatsidwa chilango chokwanira. Palibe chiwopsezo chonena za nkhondo ndi kupha chimene chidzathandiza otsutsa ameneŵa, adani a sosholizimu ameneŵa.”
Ofesala wamkuluyo ananyamula chitsulo ndi kukantha pa chimodzi cha zitinizo. Mwamuna amene anali mkati anagwera pansi chitinicho chidakali chovundikira kumutu kwake. Ndiyeno chimene chinachitika sichidzaiŵalika kwa Krupička. Iye akuti:
“Panamveka kuimba kochokera m’zitinizo. Mawu ofeŵa, pemphero lonong’ona kwa Mulungu, amene amamva kalikonse kuchokera kulikonse—ndi kuyesadi kuimba ali m’zitini zakale zadzimbirizo za uranium. Iye amakumva kwambiri kuposa nyimbo yoimbidwa m’tchalitchi chachikulu.”
Pa September 1, 1993, ntchito ya Mboni za Yehova ku Czech Republic inaloledwa mwalamulo. Mboni zachitcheki tsopano zikusangalala kuchita mwaufulu ntchito yawo yachikristu yakuphunzitsa. Inde, zili zosangalala kuuza ena za Yehova, Bwenzi lawo lalikulu koposa.
[Chithunzi patsamba 7]
Osonkhana ku Czech Republic