Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 2/1 tsamba 15
  • “Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Msonkhano Wapadera wa ku Moscow wa za Opaleshoni Yopanda Magazi
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 2/1 tsamba 15

Olengeza Ufumu Akusimba

“Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko”

MBONI ZA YEHOVA zimaonekera monga zosiyana ndi ena ndipo kaŵirikaŵiri zimanenezedwa ndi anthu ambiri chifukwa cha kukana kwawo kuikidwa mwazi. Komabe, chosankha chimenechi nchozikidwa pa Baibulo. Ilo limasonyeza kuti Mulungu amatsutsa kugwiritsira ntchito mwazi mosayenera, popeza kuti uli wamtengo wapatali m’maso mwake. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:14) Chifukwa cha kusanthula Malemba pa nkhaniyi, Mboni za Yehova zimaona kuti lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi’ moonekera bwino limaphatikizapo njira yamakono ya kuika mwazi.​—Machitidwe 15:19, 20, 28, 29.

M’zaka zaposachedwapa akatswiri a zamankhwala, pamodzinso ndi ndi makhoti m’maiko ena, achirikiza Mboni za Yehova pankhaniyi. Mwachitsanzo, ku Denmark mayi wina amene anadziŵa lingaliro la Baibulo ponena za mwazi anamwalira chifukwa cha ngozi ya galimoto. Chifukwa cha kukana kwake kuikidwa mwazi, madokotala ake anasonkhezera mkupiti wa kufalitsa nkhani zotsutsana ndi Mboni za Yehova wochitidwa ndi ofalitsa nkhani kwa mwezi wonse.

Makolo a mkazi wachichepereyu anapempha thandizo la kufufuza, ndipo mu April 1994 chigamulo chake chinalengezedwa ndi Bungwe la Madandaulo a Odwala la ku Denmark. Ilo linanena kuti wodwalayo anamwalira chifukwa cha kulephera kupereka mankhwala oyenera, osati chifukwa chakuti anakana mwazi. Chigamulo chimenechi chinazikidwa pa zofufuza za Board of Forensic Medicine ndi akuluakulu a zaumoyo. M’kalata yolembedwera zipatala zonse mu Denmark, Bungwe la Zaumoyo la Boma linanena kuti madokotala ayenera kupatsa Mboni za Yehova mtundu wina wa mankhwala abwino kwambiri amene angakhalepo, polingalira za kukana kwawo mwazi.

Chochitika china cha Dan, Mboni yazaka 15 amene anamwalira ndi matenda a leukemia. Pa chochitika chimenechi madokotala analemekeza chosankha cholimba mtima cha Dan cha kukana kuikidwa mwazi. Zimenezi zinachititsa zolankhulalankhula zambiri m’zimene ofalitsa nkhani anapatsa mlandu madokotala kuti ndiwo amene anachititsa imfa ya Dan. Komabe, ambiri sanavomerezane ndi manenanena oipawo.

Mwachitsanzo, hedimasitala wa pasukulu pamene Dan anali kuphunzira analipo pankhani ya maliro ku Nyumba ya Ufumu. Anadabwa kwambiri ndi kusimbidwa molakwika kwa nkhani ya imfa ya Dan. Atafikira mnzake wapantchito amene ali Mboni ndi mafunso ambiri ponena za Mboni za Yehova, analandira vidiyo ya Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name. Vidiyo imeneyo inamkondweretsa kwambiri kwakuti anapanga makonzedwe akuti aphunzitsi onse pasukulupo aione. Pambuyo pake, vidiyo imeneyo inasonyezedwa kwa ophunzira onse, kalasi iliyonse payokha.

Nduna ya zaumoyo ya Denmark nayonso sinavomereze mawu oipawo amene ananenedwa kwa madokotala a Dan. Iyo inanena kuti madokotala a Dan anachita chinthu choyenera povomereza chosankha chanzeru cha Dan ndi chikhulupiriro chake chozikika.

Pali olengeza Ufumu mamiliyoni ambiri amene amamvera malamulo a Mulungu. Chifukwa cha kumvera kwawo, iwo amaonekera, ‘oŵala monga zounikira m’dziko.’​—Afilipi 2:12, 15, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena