Anazichita Kaamba ka Chikondi
MKAZI wamasiye wina wokhulupirika ndi wochereza ku Canada anali kulera ana ake aakazi anayi aang’ono kuti adzakhale Akristu oona. Akulu mumpingo wake anaona kuti nyumba yake inali ndi zambiri zofunika kukonza. Iye analibe ndalama kapena luso la kuchita ntchitoyo iye mwini. Motero mogwirizana ndi lamulo lolembedwa pa 1 Timoteo 5:9, 10, akulu analinganiza mwaluntha kuti amchitire ntchitoyo. Motani?
Makonzedwe anachitidwa kuti mkazi wamasiyeyo ndi ana ake achoke panyumba kwa masiku asanu. Anthu oposa 80 mumpingo anachirikiza ndi mtima wonse, akumachita zopereka za milimo, ndalama, ndi nthaŵi. Mphindi zochepa banjalo litangochoka, antchito ofunitsitsa anabwera panyumbapo ngati njuchi. Kunja kwa nyumba konse kunakonzedwa. Makoma anakonzedwa ndi kupakidwa utoto. Pansi pake panakulungizidwa bwinobwino. Matailosi ndi kapeti zatsopano zinaikidwa. Zofunika zonse za magetsi ndi magulobu ake zinakonzedwanso. Ngakhale fanichala yoonongeka yonse inakonzedwa. Kukonza konseko kunachitidwa m’masiku asanu okha!
Mkhalidwe wa chisangalalo ndi zochitikazo unachititsa zimenezi kukhala nkhani yaikulu kumaloko. Mnansi wawo wina wazaka 80 anachita chidwi kwambiri ndi zochita za Mbonizo kotero kuti anatenga bulashi lake la penti naumirira kuti athandize. Wolemba ntchito mmodzi wa antchito odzifunira ameneŵa anapereka chokoka utsi wa m’chitofu. Wolemba ntchito wina anapereka makabati atsopano. Mwamuna wina anachita chidwi kwambiri kotero kuti anafuna kuphunzira zambiri ponena za Mboni za Yehova. Analandira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi mokondwera.
Kudabwa kwakukulu kunaonekera pankhope ya mkazi wamasiyeyo ndi ana ake atabwerera. Panali misozi, kuseka, ndi kukupatirana kochuluka—nthaŵi yosaiŵalika ya chikondi ndi malingaliro Achikristu. Indedi, chikondi chenicheni ndi nkhaŵa yosonyezedwa pa ziwalo za mpingo zosoŵa ndizo chizindikiro cha Chikristu choona, pakuti Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo apabanja la chikhulupiriro.”—Agalatiya 6:10.