Kodi Mulungu Amalamulira Dziko?
NDI pa Sande mmaŵa. Anthu ambiri amadzuka pabedi, kuvala, kudya mfisulo, ndi kuthamangira kutchalitchi. Kumeneko amamvetsera ulaliki wonena za mmene Mulungu amalamulira pa dziko lonse lapansi, wopanda wotsutsana naye pa ulamuliro. Amauzidwa kuti iye amasamalira kwambiri anthu. Nayenso Yesu Kristu amatchulidwa. Angamve kuti iye ndi Mfumu ya mafumu kwa amene bondo lililonse liyenera kupinda momvera.
Atafika kunyumba kuchokera kutchalitchi, anthu ameneŵa amatsegula wailesi yakanema ndi kumvetsera nkhani. Tsopano amamva za njala, upandu, anamgoneka, umphaŵi. Ndipo amaona zithunzi zomvetsa chisoni za anthu odwala ndi akufa.
Anthuwo angayambe kudabwa pa zinthu zimene amva kutchalitchi ndipo makamaka ponena za nkhani zimene sizinafotokozedwe kumeneko. Ngati Mulungu ali wachikondi ndi wamphamvunso, kodi nchifukwa ninji zinthu zoipa zimachitika? Ndipo bwanji nanga za Yesu Kristu? Mwachionekere, pali mawondo ambiri amene samapindidwa momumvera.
[Chithunzi patsamba 3]
Ngati Mulungu amalamulira dziko, kodi nchifukwa ninji pali kuvutika ndi chipwirikiti chotere?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Pachikuto: Chithunzithunzi cha NASA