Olengeza Ufumu Akusimba
Achichepere Akulengeza Uthenga Wabwino mu Afirika
POSAPITA nthaŵi Yesu ataukitsidwa, mwamuna wina Mwafirika anali kucheza mu Yerusalemu. Baibulo silimatchula dzina lake. Iye amangodziŵika monga “mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse.” Kodi nchifukwa ninji iye akutchulidwa m’Baibulo? Chifukwa chakuti mngelo anatsogolera mlaliki Wachikristu Filipo kuti ‘alalikire kwa iyeyo za Yesu.’ Mwamuna wa ku Aaitiopiya ameneyu anali Mwafirika woyamba m’mbiri yolembedwa kukhala chiŵalo cha mpingo Wachikristu.—Machitidwe 8:26-39.
Lerolino, pali Mboni za Yehova zikwi mazana ambiri mu Afirika. Izo zimagwiritsira ntchito mpata uliwonse kugaŵana ndi ena uthenga wabwino wonena za Yesu. Zochitika zotsatirazi zimasonyeza kuti ngakhale achichepere mu Afirika akuchita mbali yaikulu pa zimenezi.
◻ Sandy ndi Priya, atsikana aŵiri azaka 11 mu Nairobi, Kenya, anali kukhala pa nyumba zoyandikana. Iwo ankaseŵerera pamodzi ndi kubwerekana mabuku a nkhani zoŵerenga. Makolo a Priya anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsopano Priya anakala ndi mabuku atsopano owonjezera pa akale, kuphatikizapo lina limene linakhala lapamtima, Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, lofalitsidwa ndi Watchtower Society. Iye ankabwerekana buku la Mphunzitsi Wamkuru’yo ndi bwenzi lake Sandy, ndipo atsikana aŵiriwo anayamba kuliphunzira nthaŵi zonse.
Komabe, mayi wake wa Sandy, Una, anali kuloŵa tchalitchi cha Angilikani ndipo sanafune mwana wake wamkaziyo kumaŵerenga mabuku ochokera kwa Mboni za Yehova. Ngakhale kuti panali chitsutso cha mayi wake, phunzirolo linapitiriza. Tsiku lina Sandy anachonderera kwa mayi wake kuti amvetsere makambitsirano awo kamodzi kokha. Nkhani imene atsikanawo anaŵerenga tsikulo inali ya mutu wakuti “Anthu Amene Anasunga Masiku a Kubadwa.” Una anamvetsera ndipo zinamkondweretsa kwambiri. Mosataya nthaŵi, anafikira mayi wake wa Priya ndi mafunso ambiri a m’Baibulo.
Mayi wa Priya anapangana ndi Mboni ina kuti iziphunzira Baibulo ndi Una. Posapita nthaŵi Una anayamba kukambitsirana zimene anali kuphunzira ndi mnzake wa pantchito Dolly. Panthaŵiyi, Priya wazaka 11 anapitabe patsogolo naganiza za kusonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Pamsonkhano umenewo, Priya anakondwa chotani nanga kuona kuti nayenso Una ndi Dolly anabatizidwa!
◻ Pali maiko ena a mu Afirika kumene ntchito ya Mboni za Yehova sili yolembetsedwa. M’dziko lina lotero, muli mkhalidwe wosasamala kwambiri za ntchito za chipembedzo ndi zikhulupiriro za Mboni. Pasukulu ina m’dzikolo, kamnyamata ka zaka zisanu ndi ziŵiri ndi mphwake wazaka zisanu ndi chimodzi—ana a Mboni—analoledwa kuchokapo panthaŵi ya mapemphero a chipembedzo.
Tsiku lina mphunzitsi watsopano analamula kuti anyamatawo akhalepo ndi kupemphera pamodzi ndi ana ena. Mnyamata wamkulupoyo anakana ndipo anakwapulidwa ndi mphunzitsiyo. Mphwakeyo, Shadrack wazaka zisanu ndi chimodzi, anaumirira kuti aonane ndi hedimasitala mu ofesi mwake. Hedimasitala ndi mphunzitsi watsopanoyo anafunsa chifukwa chake iye anakana kugwirizana ndi ena. Anamfunsa ngati anawopa kukwapulidwa ndi makolo ake. Iye anayankha m’Chiarabu chabwino kwambiri kuti: “Iyayi, Mulungu amene ndimamlambira sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere. Sindingakhale mmodzi wa Mboni za Yehova kunyumba ndi wa chipembedzo china kusukulu!” Chotulukapo, analoledwa kusamakhalapo.
Atabatizidwa, mwamuna wa ku Aaitiopiya wotchulidwa m’buku la Machitidwe “anapita njira yake wokondwera.” (Machitidwe 8:39) Lerolinonso, olengeza Ufumu m’kontinenti yaikulu ya Afirika akusangalala ndi mwaŵi wawo wa ‘kulalikira za Yesu.’—Machitidwe 8:35.