Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 3/15 tsamba 31
  • Yehova Adzapulumutsa Dziko Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Adzapulumutsa Dziko Lapansi
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 3/15 tsamba 31

Yehova Adzapulumutsa Dziko Lapansi

BWALO LA NDEGE lokhala pachisumbu cha Maldives limatsekedwa kwa maola angapo tsiku lililonse. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti madzi osefukira amafika m’msewu wa ndege, akumachititsa kukhala kovuta kuti ndege zitere. Asayansi ena akuwopa kuti mlingo wa madzi a nyanja pa zisumbu za Maldives ungakwere kwa pafupifupi mita imodzi m’zaka zana limodzi zilinkudza. Ngakhale kuti umenewu ukuoneka kukhala mlingo waung’ono kwambiri, kuwonjezeka koteroko kungafafanize kotheratu maiko apachisumbu asanu ndi aŵiri padziko. Ndithudi, malinga ndi kunena kwa UN Chronicle, kuwonjezeka kwa mamita aŵiri kungaphimbe chiungwe cha zisumbu chonsecho, zisumbu pafupifupi 1,200!

Kodi nchiyani chimene chikuchitisa kukwera kwa mlingo wa madzi a nyanjako? Malinga ndi kunena kwa UN Environment Program, kuipitsa thambo la dziko lapansi kochititsidwa ndi “mipweya yotentha thambo” kumachititsa nyanja zokhala m’malo ofunda kusefukira, kusungunuka kwa nsonga za zitunda za madzi oundana ndi madzi oundana oyenda, ndipo motero, mlingo wa madzi a nyanja umakwera. Panos Institute yokhala ku London ikunena kuti kuipitsa thambo “kungakhale kumene kwachititsa tsoka lofika pang’onopang’ono limene likusintha malire enieniwo a mtunda ndi nyanja.”

Kufunda kwa dziko lapansi kudakachititsabe mkangano pakati pa asayansi. Komabe, ife tingakhale otsimikizira kuti mavuto apadziko sadzaletsa chifuniro cha Mulungu. “Dziko lokhalamo anthu lomwe lidzakhazikika,” limatero Baibulo. ‘Silidzagwedezeka.’ (1 Mbiri 16:30) Yehova ali ndi mphamvu pa malo a dziko lapansi, ndipo tiyenera kusangalala kuti posachedwapa adzapulumutsa dziko lapansi ndi anthu omwe kuti asawonongeke.​—Salmo 24:1, 2; 135:6; 2 Petro 3:13.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Chojambulidwa ku chithunzi cha NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena