Laling’ono Koma Lamphamvu
ROBERT, mnyamata wa ku Canada, anapita paulendo mu Ulaya yense akumafunafuna chifuno cha moyo wake. Anaona zinthu zambiri zimene zinamtayitsa chiyembekezo cha mtsogolo.
Pamene anali khale m’kantini ina ku Seville, Spain, Robert anapatsidwa trakiti lina lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Poyamba, Robert anakayikira. “Komabe, ndinaliŵerenga,” iye anatero. “Sinditha kufotokoza chimene chinachitika, koma ndinaona kuti linali kunena zomveka. Paulendo wanga, ndinali nditaona kupsinjika maganizo kwa anthu ndi chisoni chawo zamitundu yambiri, ndipo ndinakhumudwa chifukwa cha kusakhoza kwanga kusintha zinthu. Nditaŵerenga trakitilo, ndinalingalira kuti, ‘Kodi “dziko latsopano” limeneli likhoza kukhalako?’ Ndiyeno ndinati, ‘Inde, mwina lidzakhalako.’”
Pokhala atapezanso chiyembekezo, Robert analembera ofesi ya Mboni za Yehova ku Canada, akumapempha kuti wina akamchezere atabwerera kwawo ndi kumthandiza kumvetsetsa Baibulo.
Mosakayikira, mawu olankhulidwa ngamphamvu. Komabe, musachepse mphamvu ya uthenga wosindikizidwa. Si kanthu kuti zili zazing’ono, zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo zili ndi chikoka champhamvu. Zimakhudza maganizo ndi mtima, zikumapereka chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo.—Ahebri 4:12.