Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 12/1 tsamba 32
  • Mawu Ochirikiza Chikhulupiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Ochirikiza Chikhulupiriro
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 12/1 tsamba 32

Mawu Ochirikiza Chikhulupiriro

PAMENE zaka za zana lapitalo zinatha, mawu ochirikiza sayansi, nthanthi, ndi kukana chipembedzo anali kuwononga chikhulupiriro mwa Mulungu ndi kuuziridwa kwa Baibulo.

Koma amenewo sanali mawu okha amene anamvedwa. Ofufuza ambiri anaona kuti panali zambiri zimene zikananenedwa mochirikiza chikhulupiriro mwa Mulungu mmalo mwa kuchirikiza kukana Mulungu. Zopenda zawo zinasonyezanso umboni wambiri wakuti Baibulo lili Mawu a Mulungu ouziridwa.

Liwu lina lotchuka kwambiri linali la C. T. Russell. Mamiliyoni anaŵerenga voliyumu yake ya 1886 ya The Divine Plan of the Ages. Mutu wina wofotokozedwa mwamphamvu mmenemo unali wakuti “Kukhalapo kwa Mlengi Wanzeru Wamkulukulu Kwatsimikiziridwa.”

M’zaka makumi ena zotsatira, Russell analemba nkhani, matrakiti, ndi mabuku amene anapereka zifukwa zamphamvu zokhulupirira Mulungu ndi Baibulo. Zimenezi zinafalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Pulezidenti wake wachiŵiri, J. F. Rutherford, analemba Creation (1927) ndi mabuku ena amene amawonjezera pa liwulo lochirikiza chikhulupirirocho.

Posachedwapa sosaite imeneyo yakonza chidziŵitso chatsopano chonena za nkhani zimenezi. Mboni za Yehova zingapereke chimenechi kotero kuti muchipende mosamalitsa.

Ngati mungafune kudziŵa zochulukirapo kapena ngati mungafune kuti munthu wina afike kwanuko kudzayamba nanu phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka, 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 2.

[Zithunzi patsamba 32]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena