“Ndi Mmene Akristu Oona Ayenera Kukhalira”
M’BUKU lake la 1990 la Arbeit macht tot—Eine Jugend in Auschwitz (Ntchito Imakupha—Unyamata mu Auschwitz), Tibor Wohl wopulumuka ku Auschwitz akulemba za kukambitsirana kumene anamva pakati pa akaidi anzake aŵiri. Winayo, wa ku Austria, ananena kuti anali “wosakhulupirira.” Komabe, anayamikira akaidi amene anavala chizindikiro chotchedwa purpletriangle—Ophunzira Baibulo, mmene Mboni za Yehova zinkatchedwera m’misasayo.
“Iwo samapita kunkhondo,” wa ku Austria anatero kwa mnzake. “Iwo angakonde kuphedwa m’malo mwa kupha munthu wina aliyense. Malinga ndi kuganiza kwanga, ndi mmene Akristu oona ayenera kukhalira. Leka ndikuuze nkhani yosangalatsa kwambiri imene inachitika pamene ndinali nawo. Tinali pamodzi ndi Ayuda ndi Ophunzira Baibulo omwe m’nyumba imodzi mumsasa wa Stutthof. Masikuwo Ophunzira Baibulo anali kuchitira ntchito yachilango panja pozizira kwadzaoneni. Sitinamvetsetse mmene anapulumukira. Iwo ananena kuti Yehova anawapatsa nyonga. Iwo anafunikira mkate wawo kwambiri, chifukwa chakuti anali ndi njala. Koma kodi udziŵa zimene anachita? Iwo anasonkhanitsa mkate wonse umene anali nawo, nadya theka lake nagaŵira abale awo theka linalo, abale awo auzimu, amene anachokera kumisasa ina ali ndi njala yofa nayo. Ndipo anawalandira ndi kuwapsompsona. Asanadye, anapemphera, ndipo pambuyo pake nkhope zawo zinali zachimwemwe. Ananena kuti palibe yemwe analinso ndi njala. Chotero, ineyo ndinaganiza kuti, ‘Ameneŵa ndi Akristu oona.’ Ndi mmene ndinaganizira nthaŵi zonse kuti ayeneradi kukhala otero. Kukanakhala bwino chotani nanga kulandira mabwenzi anjala mwanjira imeneyo muno mu Auschwitz!”