Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 3
  • Kodi Mumaona Baibulo Kukhala Lofunika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumaona Baibulo Kukhala Lofunika?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • “Ndinetu Kapolo wa Yehova!”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Sanafooke Chifukwa cha Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 3

Kodi Mumaona Baibulo Kukhala Lofunika?

ZAKA zoposa 200 zokha zapitazo, Mary Jones anabadwa mu Llanfihangel, mudzi wakutali wa ku Wales pafupi ndi gombe la Atlantic. Makolo ake anali amphaŵi owomba nsalu​—osauka kwambiri kwakuti analibe Baibulo. Koma analoŵetsa mwa mwana wawo chikondi cha Mulungu mwa kumuuza nkhani za Baibulo ndi kubwereza malemba amene anawakumbukira. Kaŵirikaŵiri Mary anali kuŵerenga Baibulo la Chiwelsh la mnansi wake ndipo anayamba kusunga ndalama zochepa zomwe anapeza, ali wotsimikiza mtima kudzagula lakelake.

M’chaka cha 1800, pamene Mary anali ndi zaka 16, anamva kuti Mabaibulo angapo a Chiwelsh anali kugulitsidwa m’tauni yaing’ono ya Bala pa mtunda wa makilomita 40. Molimba mtima, anatsimikiza kupita kumeneko. Iye anayenda pansi wosavala nsapato, akumadutsa mapiri. Komabe, panthaŵi imene anafika kumeneko, makope onse anali atagulitsidwa. Mary anamvanso kuti ndalama zimene anasunga zinali zochepa kwambiri.

Pasitala wa kumaloko anachita chidwi kwambiri ndi chidziŵitso cha Mary ndi kukonda kwake Baibulo. Pomuona akulira chifukwa cha kugwiritsidwa mwala pambuyo pa kuyesayesa konse kumene anapanga, mokoma mtima anampatsa kope lake la iyemwini, akumati: “Liŵerenge mosamalitsa, liphunzire mwakhama, sunga mawu opatulikawo m’mumtima mwako, ndipo chita mogwirizana ndi ziphunzitso zake.”

Nkhani imeneyi inasimbidwa pambuyo pake pa msonkhano wa Committee of Religious Tract Society of London. Kumeneko anapanga chosankha cha kupereka matembenuzidwe a Baibulo osati kwa anthu a ku Wales okha koma padziko lonse. Kuchokera pa chiyambi chaching’ono chimenechi panabuka loyambirira la mabungwe ambiri a Baibulo a m’zaka za zana la 19. Pambuyo pake, makope a zinenero zina a Baibulo anayamba kupezeka ochuluka.

Lerolino, Watch Tower Bible and Tract Society, yokhazikitsidwa mu 1884, imasindikiza Mabaibulo ndi zothandizira kuphunzira Baibulo m’zinenero zoposa 200. Padziko lonse, yagaŵira makope 72 miliyoni a New World Translation of the Holy Scriptures ya chinenero chamakono. Pokhala yotembenuzidwa kuchokera ku Chihebri ndi Chigiriki choyambirira, tsopano New World Translation ilipo yathunthu kapena mbali yake ina m’zinenero 18 ndipo pakali pano ikutembenuzidwa m’zinenero 12 zowonjezereka.

Popeza kuti tsopano Baibulo limapezeka pafupifupi kwa aliyense, kodi mumaliona motani? Kodi mumaona Baibulo kukhala lofunika? Kodi muli ndi kope limene mumaliona kukhala lamtengo wake ndi kuliŵerenga?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

From the book The Story of Mary Jones and Her Bible

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena