Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/15 tsamba 11
  • Akristu Achangu a ku Britain

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu Achangu a ku Britain
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amalalikira Kunyumba ndi Nyumba?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!
    Galamukani!—1988
  • Akristu Onse Oona Amalalikira
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/15 tsamba 11

Akristu Achangu a ku Britain

Malinga nkunena kwa The Economist, ochepera pa 10 peresenti ya anthu 56 miliyoni a ku Britain ali Akristu achangu tsopano lino. Pa Sande iliyonse, anthu ochepera pa mamiliyoni anayi amapita kutchalitchi. Mwa ameneŵa, 1.1 miliyoni okha ndiwo a Anglican. Komabe, mosasamala kanthu za kukayikira kukhalako kwa Mulungu kofala, Tchalitchi cha England chikupitiriza ndi malo ake monga chipembedzo cha Boma. “Kwa zaka zambiri Britain sali chitaganya Chachikristu koma amakana kuvomereza kukayikira kukhalako kwa Mulungu, kwakukulukulu chifukwa cha kukondetsa mwambo,” akutero magazini ankhani amodzimodziwo. Nkosadabwitsa kuti andale amakono ndi manyuzipepala akufuna kudzilekanitsa kwa Tchalitchi, kutha kwa unansi pakati pa Tchalitchi ndi Boma.

“Dziko limene lili lachikunja, limene limadzinenera kukhala Lachikristu, ndidziko loipa koposa,” anadandaula motero Walter Bagehot, mkonzi wa The Economist wa m’zaka za zana la 19. Koma m’zaka za zana loyamba C.E., Yesu Kristu ananena kuti ophunzira ake sanali ‘a dziko lapansi, monga iye sanali wa dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Komabe, iye anawatumiza m’dziko kukalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mofananamo lerolino, Mboni za Yehova padziko lonse nzotchuka chifukwa cha kulalikira mwachangu “pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.”​—Machitidwe 20:20.

Poziyerekezera ndi a Anglican, Mboni 126,173 za ku Britain nzoŵerengeka. Koma zimathera pafupifupi maola 20 mwezi uliwonse pamisonkhano Yachikristu. Ndiponso, mu 1992 Mboni iliyonse inathera avareji ya maola 16 owonjezereka pamwezi ikulengeza kwa ena mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, boma limene posachedwapa lidzakhazikitsa dziko latsopano lolungama. (Mateyu 24:14; 2 Petro 3:13) Nthaŵi yotsatira pamene Mboni za Yehova zidzakuchezerani panyumba panu, kodi mudzamvetsera uthenga wawo wapadera ndi kudziŵa chimene chimasonkhezera changu chawo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena