Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 9/1 tsamba 32
  • Madzi a Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madzi a Moyo
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 9/1 tsamba 32

Madzi a Moyo

“WAKUMVA anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) “Madzi a moyo”​—amene amatanthauza makonzedwe onse a Mulungu kaamba ka chipulumutso chathu ozikidwa pansembe yadipo ya Yesu Kristu. Makonzedwe ameneŵa alipo, ndipo ngaulere. Ha, ndi kuoloŵa manja kwabwino chotani nanga kwa Mulungu wathu! Komabe, kodi madziwo amaphiphiritsira chiyani?

Eya, madzi enieni amatheketsa zomera kukula m’nthaka, ndipo zimenezo zimatheketsa anthu kukhala ndi moyo. Popanda madzi, zomera, ndi anthu omwe sangakhaleko. Ndiponso, thupi lanu lili ndi 65 peresenti ya madzi. Akatswiri ena azaumoyo amavomereza kuti nkwabwino kusunga kuchuluka kwa madzi kumeneko mwakumwa pafupifupi 2.4 lita ya madzi patsiku. Ntchito zonse za mkati mwa thupi lanu​—kuyambira pa kupukusa zakudya ndi kutaya zoipa za m’thupi​—zimafuna madzi. Tangoyesani kukhala mlungu umodzi osamwa madzi, ndipo mudzafa.

Mofananamo, “madzi a moyo” amatheketsa ndi kuchilikiza moyo wauzimu. Ngati tikana madzi a moyo, tilibe mtsogolo mokhalitsa. (Yohane 3:36) Ngati tiwalandira, tingakhale ndi moyo wosatha. Nzosadabwitsa kuti mkazi Wachisamariya anayankha motenthedwa maganizo pamene Yesu anamuuza kuti: “Iye wakumwa madzi amene ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthaŵi zonse; koma madzi amene ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha”! (Yohane 4:14) Tiyesetsetu mofunitsitsa ndi kutenga madzi a moyo kwaulere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena