Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/1 tsamba 31
  • Zipatso za Umboni wa Mwamwaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zipatso za Umboni wa Mwamwaŵi
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/1 tsamba 31

Zipatso za Umboni wa Mwamwaŵi

IMODZI ya mbali zokondweretsa kwambiri za utumiki Wachikristu m’Honduras ndiyo umboni wa mwamwaŵi. Kukambitsirana kwa timagulu ta anthu pamisika, m’zipinda zodikirira madokotala, m’sitima, ndi pokwerera basi ndiko umoyo wa m’Honduras. Zimenezi zimakupangitsa kukhala kosavuta kufikira anthu mwamwaŵi ndi nkhani ya m’Baibulo.

Mumzinda wa Omoa, munali kukhala mkazi wina amene sanafune Mboni za Yehova mpang’ono ponse. Iye sanali kulankhula nazo kapena kuvomera mabuku awo. Komabe, anali wokonda kupeza ndalama kwambiri, motero anali kuŵeta nkhuku. Podziŵa mkhalidwe wake, mbale wina analankhula naye mwamwaŵi ponena za njira zina zimene angasungire nthaŵi ndi ndalama zomwe poŵeta nkhuku. Iye anakonda kwambiri kumva zimenezi. Pambuyo pamasiku oŵerengeka, magazini a Galamukani! anatulutsa nkhani yonena za kusunga nthaŵi ndi ndalama, chotero mbaleyo anatenga kope limodzi ndi kupatsa mkaziyo. Iye analiyamikira kwambiri, ndipo tsopano akulandira mabuku athu mwachisangalalo.

Mlongo wina amene anali kugwira ntchito m’sitolo anachita mantha ndi maonekedwe a kasitomala wachichepere wina wa tsitsi lalitali kwambiri. Iye analimbika mtima nalankhula naye ponena za chiyembekezo cha Paradaiso, koma iye anayankha mwamwano kuti sakhulupirira nthano zopanda pake ndi kuti anali wopulupudza ndi womwerekera ndi anamgoneka. Mlongoyo analimbikira kulalikira mwachidule kwa mnyamatayo nthaŵi zonse pamene anabwera. Nthaŵi ina analongosola kwa iye kuti malinga ndi 1 Akorinto 6:9-11, chinthu chofunika ndicho chimene umakhala, osati chimene unali. Pamene mnyamatayo anafunsa zimene mlongoyo anaganiza ponena za tsitsi lake lalitalilo, mlongoyo anayankha kuti analibe ulamuliro pa tsitsi la munthu aliyense, koma kuti anakhulupirira chiphunzitso cha Baibulo chakuti tsitsi lalitali linyozetsa mwamuna. (1 Akorinto 11:14) M’maŵa mwake, iye anali wometa mwaudongo ndipo anali ndi tsitsi lalifupi! Anapempha phunziro la Baibulo, ndipo mbale wina anavomereza mokondwera. Tsopano iye ngwobatizidwa ndipo akuchititsa maphunziro akeake.

Kamnyamata kachichepere kena kanali ndi chizoloŵezi cha kulankhula kwa aliyense amene kanakumana naye, monga momwe achichepere ambiri a zaka zisanu ndi ziŵiri amachitira. Kataona mwamuna wina atakhala pakhonde la nyumba yake atagwira buku, kamnyamatako kanafunsa ngati buku limene anali kuŵerengalo linali Baibulo. Katadziŵa kuti silinali Baibulo​—ndipo linali buku la zaumakanika​—kanauza mwamunayo motsimikiza kuti moyo wosatha angaupeze kokha mwakuŵerenga Baibulo mosamalitsa. “Ngati mufuna, atate angaphunzire nanu,” iko kanatero, ndipo kanapereka mwamunayo kunyumba kwawo kukawonana ndi atate wake. Mbali yosangalatsa ya nkhaniyi njakuti mwamunayu anabatizidwa mu 1976. Zinadzadziŵika kuti zaka zambiri kalelo, anali atalandira magazini kwa mlongo wina koma anatayana naye. Ha, umboni wa mwamwaŵi ngwofunika chotani nanga!

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena