Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 11/1 tsamba 32
  • Anapata Mphotho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anapata Mphotho
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 11/1 tsamba 32

Anapata Mphotho

“NDIKUTHOKOZANI,” akutero Kiyoe, wakalasi lapamwamba pasukulu yasekondale, polembera ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Japan. Kodi nchiyani chimene iye akuyamikira kwambiri? Posachedwapa Kiyoe anapata mphotho yaikulu koposa mumpikisano wa kulemba chimangirizo cha nkhani, wochirikizidwa ndi Japan Traffic Safety Association. Mfupo yamtengo wapatali imeneyo inaphatikizapo ulendo wa ku Sweden.

Kiyoe analemba kalata yosonyeza chiyamikiro chake kaamba ka mabukhu ambiri abwino kwambiriwo ofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society, amene iye akuganiza kuti anamthandiza kwambiri kupambana. Kuwonjezera pa mpikisano umenewu, iye waimira sukulu yake m’mipikisano yambiri yakulankhula ndi yolemba zimangirizo za nkhani. “Mu yochuluka ya mipikisano imeneyi,” iye akutero, “mutu wankhani umaperekedwa, ndipo ana a sukulu amaufufuza mulaibulale kuti alembe zimangirizo za nkhani zawo. Komabe, sindimavutika ndi kuchita zonsezo. Ndimapeza nkhani zabwino kwambiri pashelufu ya mabukhu kunyumba!” Iye akupitiriza kuti: “Mosasamala kanthu kuti ndimutu wotani, kaya ukhale mavuto aukalamba, malo okhala, maunansi ndi maiko akunja, kapena kudziwongolera, kaŵirikaŵiri mumakhala nkhani zolembedwa bwino m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!”

Komabe, simabukhu okha amene athandiza Kiyoe. Iye akunena kuti maphunziro amene analandira kupyolera mwa maprogramu akuphunzira a Mboni za Yehova anamthandiza kuwongolera kuŵerenga ndi kulemba kwake, ndipo zimenezi zinamkhozetsa kupambana m’mipikisanoyo. “Panthaŵi ina, ndinafunitsitsa maphunziro apayunivesite,” iye akuvomereza motero. “Koma kodi nkuti kumene ndingapeze maphunziro onga ameneŵa?” Tsopano akuyembekezera kudzagwira ntchito yanthaŵi yonse yothandiza ena kupindula ndi maphunziro amene iye walandira. Pamene akusangalala ndi mphotho ya kulemba nkhani, mtima wa Kiyoe ngwotsimikiza kudzapata mphotho ya moyo.​—Yerekezerani ndi Afilipi 3:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena