Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 10/15 tsamba 3
  • Banja Liukiridwa!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Banja Liukiridwa!
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Banja—Nlofunika kwa Munthu Aliyense!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mavuto A Banja—Chizindikiro cha Nthaŵi
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Pamene Ndewu Ibuka m’Banja
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 10/15 tsamba 3

Banja Liukiridwa!

“BANJA ndilo chigwirizano chaumunthu chakale koposa. Nlofunika koposa m’njira zambiri. Ndilo phata lofunika koposa la chitaganya cha anthu. Kutsungula konse kwakhalapo kapena kwazimiririka, zikumadalira pakulimba kwa moyo wabanja kapena kufooka kwake.”

Inatero The World Book Encyclopedia kalero mu 1973. Komabe, malinga nkalingaliridwe ka lerolino, mawu amenewo amamvekera mochititsa mantha, pafupifupi atsoka. Zaka zoŵerengeka zapitazo zawona chimene chakhala kuukiridwa kwapoyera pamoyo wabanja. Mlangizi wodziŵika John Bradshaw akulemba kuti: “Lerolino m’banja muli chipwirikiti. . . . Kuwonjezereka kwa zisudzulo, ziwawa za achichepere, kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala molakwa kwakukulu, mliri wa kugonana kwapachibale, kudya mosalongosoka ndi kumenya ndizo umboni wakuti kanthu kena nkolakwika kwambiri.”

Ndithudi, “umboni wakuti kanthu kena nkolakwika kwambiri” m’banja ungapezeke m’dziko lonse. Ponena za mkhalidwewo mu Ulaya The Unesco Courier inati: “Chiyambire 1965, pakhala kuwonjezereka kwakukulu m’chiŵerengero cha zisudzulo pakontinenti yonseyo. . . . [Pakhala] kuwonjezereka m’chiŵerengero cha mabanja a kholo limodzi.” Mofananamo maiko osatukuka akukhala ndi chiwonjezeko cha mavuto a banja. Mlembiyo Hélène Tremblay akuti: “Kwa mamiliyoni ambiri a anthu okhala m’zitaganya zimene kwa zaka mazana zakhala ndi njira ya moyo yokhazikika, yodziŵika mtsogolo mwake, yosasinthasintha kwa zaka mazana ambiri, lerolino ndiyo nthaŵi ya chisokonezeko.”

Makamaka chochititsa mantha kwambiri ndicho mkhalidwe umene ulipo m’mabanja ambiri lerolino. Mu United States mokha, mamiliyoni ambiri a ana amaleredwa ndi kholo lauchidakwa. Pakhalanso kuwonjezereka kowopsa m’chiwawa cha m’banja. M’bukhu lawo lakuti Intimate Violence, ofufuzawo Richard Gelles ndi Murray Straus akusimba kuti: “Mwachiwonekere mungaukiridwe, kumenyedwa, ndi kuphedwa m’banja mwanu mwenimwenimo ndi wokondedwa kuposa malo ena alionse, kapena ndi wina aliyense m’chitaganya chathu.”

Ngati kwenikwenidi kukhalapo kwa kutsungula kukudalira pakulimba kwa banja, pali chifukwa chochitira nkhaŵa ndi mtsogolo mwa kutsungula. Chikhalirechobe, mtsogolo mwa kutsungula sindimo mmene mungakhale nkhaŵa yanu kwenikweni. Mwachiwonekere kwambiri nkhaŵa yanu ndiyo zimene chipwirikiti chimenecho chingatanthauze ku banja lanu. Kodi chotulukapo chidzakhala chotani? Yankho lake lochokera kumagwero odalirika lingakudabwitseni kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena