“Zakumwamba Zimalalikira . . . ”
Pafupifupi makilomita mamiliyoni 150 kuchokera pamene muli tsopanoli, dzuŵa likuŵala ndi kuunika kwamoto mumlengalenga. Ngakhale kuti lalambiridwa kwa zaka mazana ambiri, mnansi wathu wakumwambayo waulemerero, ali umboni wa mphamvu ya Mlengi wake, “Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 115:15) Kuunika kwake ndi kutentha kuli kofunika kaamba ka moyo padziko lapansi. Ndipo zimene asayansi aphunzira ponena za ilo zimatizizwitsa.
Iwo amatiuza kuti dzuŵa limatulutsa mphamvu yochuluka yodabwitsa. Kodi mumazindikira kuti kambali kochepera pa theka la mbali imodzi mwa mbali mamiliyoni chikwi chimodzi za kutentha ndi kuunika kumene limatulutsa ndiko kamatsekerezedwa ndi dziko lapansi? Komabe, kambali kochepa kameneko kamakwanira mphamvu yochita 240,000,000,000,000 horsepower pamphindi iriyonse!
Kodi ndimotani mmene dzuŵa limapangira mphamvu yakutentha yonseyo? Mwakugwiritsira ntchito ng’anjo ya moto wa maatomu m’chitima chake imene imatulutsa mphamvu mwa kutentha pafupifupi matani ametriki a hydrogen 3.6 miliyoni m’kamphindi kamodzi. Mokondweretsa, kaamba ka kukhalapo kwa anthu, dzuŵa liri ndi mphamvu yokwanira yakupitiriza mchitidwe umenewu kwa zaka zikwi mamiliyoni zikwi zambiri ambirimbiri.
Zinthu zina zimene asayansi atulukira zimadzutsa mafunso owonjezereka. Mwachitsanzo, dzuŵa likunjenjemera mosalekeza, mofanana ndi chitsulo chomenyedwa ndi nyundo. Chifukwa ninji? Ndiponso, talingalirani izi: Chitima choyaka moto cha dzuŵa ndicho mbali yotentha koposa ndipo pamene muyalo uli wotalikirana ndi chitimacho, umakhalanso wopolerapo. Koma pamene tifika kumuyalo wakunja wa thambo lozungulira dzuŵa, wotchedwa corona, zimenezo zimasintha. Muyalo wa corona ngwotentha kuposa miyalo yapafupi ndi chitima choyaka motocho. Chifukwa ninji?
Ndiponso, pamene—mofanana ndi dziko lapansi—dzuŵa likuzungulira, mbali zake zosiyanasiyana zimazungulira paliŵiro losiyanasiyana. Mwachitsanzo, muyalo wakunja umazungulira mofulumirapo kuposa miyalo yamkati. Chifukwa ninji? Ndipo kodi zimenezo nzotheka motani? Kenako, pali masunspot. Mobwerezabwereza, maŵanga apadzuŵa ameneŵa amabwera ndi kupita mokhazikika panyengo ya zaka 11. Kodi nchifukwa ninji amasintha mokhazikika chotero?
Ngakhale kuti pali zambiri zoti ziphunziridwe ponena za dzuŵa, zimene tikudziŵazo zimatichititsa kulemekeza Mlengi wake, Yehova. Nthaŵi iriyonse pamene tiwona dzuŵa, timakumbutsidwa kuti “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo liwonetsa ntchito ya manja ake.”—Salmo 19:1.