Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/15 tsamba 31
  • Njira ya Kubwereranso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Kubwereranso
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/15 tsamba 31

Njira ya Kubwereranso

‘ANANENA nawo mwa mafanizo.’ Baibulo limayamba motero kufotokoza mafanizo atatu a Yesu okumbukika onena za chifundo​—la nkhosa yotayika, ndalama yotayika, ndi la mwana woloŵerera.​—Luka 15:3-32.

Nkhani ziŵiri za m’Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, zinafotokoza mafanizo amenewo ndi kuthandiza oŵerenga ambiri kuwona mmene chifundo chingaperekedwere lerolino. Chisamaliro chachikulu chinasumikidwa pa abusa auzimu m’kuyambirira kuwonana ndi anthu amene anachotsedwa m’gulu komabe amene angalabadire maulendo okoma mtima ameneŵa. Kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo cha nkhani zimenezi ndi njira yatsopanoyo?

Mwamsanga magaziniwo atafalitsidwa, mwamuna wina m’chigawo cha Washington, U.S.A., analemba kuti: “Umboni wa kukoma mtima kwa chikondi chosayerekezeka cha Yehova wandifikira lero ndi positi. Ndakhala pano misozi iri m’maso mwanga ndi chisangalalo mumtima mwanga pamakonzedwe ndi masinthidwe operekedwa ndi Wammwambamwambayo. Ndi Mulungu wowona ndi wachilungamo yekha amene angathe kupereka chithandizo kwa anthu onga nkhosa amene atayika. . . . Indedi, ndine wochotsedwa mumpingo koma ndiri mkati mwa kuti ndibwezeretsedwe.” Mu October iyeyu anabwezeretsedwanso.

Koma bwanji za maulendo ochitidwa ndi akulu ena aŵiri a mpingo? Mkazi wina Wachikristu analemba kuti: “Mawu sangathe kufotokoza mmene ndikumvera. Mwamuna wanga wakhala atachotsedwa mumpingo kwapafupifupi zaka 13. Akulu anamfikira, monga momwe nkhaniyo inaperekera lingaliro. Usiku wathawu kwanthaŵi yoyamba m’zaka zambiri, anamka kuumodzi wa misonkhano. Tsopano iye akuyesa kusintha moyo wake ndi kubwerera.”

Pamene oyang’anira oyendayenda amachezera mpingo ndi mpingo, iwowa amawona zotulukapo zake. Posachedwapa woyang’anira dera wina analemba kuti:

“Pamene Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991 inafalitsidwa, ambiri anadabwa za chimene chikakhala kulabadira kwa kuchezera kwa akulu. Yankho lake lakhala lachiwonekere kwambiri.

“M’dera lathu, mipingo inayi yotsiriza imene ndachezera yawona kubwereranso ku Nyumba Yaufumu kwa anthu asanu ndi anayi. Ngakhale kuli kwakuti mmodzi yekha wabwezeretsedwa, asanu ndi atatu enawo akupanga kupita patsogolo kwabwino kwambiri. Akulu ndi mipingo amakondwera kuwona zipatso za ntchito yawo ndi nzeru ya kugwiritsira ntchito zitsogozo zateokratiki.

Tikusangalala ndi makonzedwe abwino ameneŵa, achifundo. Monga momwe mlongo wina wobwezeretsedwa ananenera kuti, ‘mwa ine ndekha ndinalibe mphamvu ya kubwerera, popeza kuti ndinalingalira kukhala wotsutsidwa pamaso pa Yehova. Koma pamene akulu anafika, chinali chilimbikitso chimene ndinafuna cha kubwerera.’ Kutenthedwa maganizo kwake kwalimbikitsa mpingo kwambiri.”

Ngakhale ngati ambiri amene amafikiridwa salabadira, zabwino zikuchitidwadi mwa kuyamba kufikira kumeneku kwachifundo. Motero, kuyambira mu September akulu mumpingo uliwonse adzapenda maina a awo okhala m’gawo lawo amene ali ochotsedwa mumpingo ndipo adzalinganiza kuyendera awo onse amene akuwalingalira kuti angalabadire chifundo choperekedwacho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena