Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/15 tsamba 8-9
  • Kuchokera ku Chipatala Chotchuka Kumka ku Nyumba Yaufumu Yapadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera ku Chipatala Chotchuka Kumka ku Nyumba Yaufumu Yapadera
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/15 tsamba 8-9

Kuchokera ku Chipatala Chotchuka Kumka ku Nyumba Yaufumu Yapadera

MU 1770 Mngelezi wina wotchuka wotumba maiko Lieutenant James Cook anali mmalinyero wa ngalaŵa yolemera matani 369 yotchedwa Endeavour mmbali mwa gombe lakummaŵa losatumbidwa la Australia. Madzulo ena a June 11, chombocho chinagunda mwala wa korali mmbali mwa nyanja kudera lakutali cha kumpoto kwa kontinentiyo. Ngalaŵa yamatabwa a oak inawonongeka kwambiri. Kukonza kunali kofunika mwamsanga ngati amalinyerowo anati akapulumuke. Mathiriro amtsinje wapafupiwo anakhaladi malo abwino a kukonzerako, kumene kunatenga masabata asanu ndi limodzi. Zaka zana limodzi mphambu zitatu pambuyo pake, golidi anatumbidwa m’chigawochi. Kufunafuna golidi kunayambika! Anthu zikwi makumi ambiri anadza kudzayesa ngati angampeze. Ndimo momwe Cooktown anabadwira.

Mu 1879 chilolezo cha boma chinaperekedwa kumanga chipatala chachikhalire chosamalira odwala ndi ovulala m’ngozi za m’migodi. M’chaka chomwecho, kumbali ina ya dziko, July 1 anawona kope loyamba la magazini a Zion’s Watch Tower. Chiyambire pamenepo, magazini ameneŵa agaŵira programu ya thanzi lauzimu kwa mamiliyoni a anthu owopa Mulungu. Panthaŵiyotu sikunadziŵike kuti nyumba ya chipatala cha Cooktown tsiku lina ikakhala yogwirizanitsidwa ndi magazini ameneŵa.

Zaka zoposa zana limodzi zitapita, Chipatala cha Cooktown chinafunikira kuloŵedwa m’malo ndi china. Ndalama za boma zomangira nyumba yatsopanoyo zinalipo, chotero makampani osamutsa chipatala chakalecho anapemphedwa. National Trust of Queensland inakondweretsedwa ndi nyumba yotchuka imeneyi. Komabe, mtengo wa kusamutsira malo ena ndi kukonzanso nyumbayo unalidi wokwera kwambiri. Palibe amene anadzipereka kudzachita ntchitoyo.

Pafupifupi panthaŵi yofananayo, mpingo wina waung’ono wa Mboni za Yehova mu Cooktown unali kufunafuna malo achikhalire ochitira misonkhano Yachikristu. Unalibe malo ndipo unali ndi $A800 zokha. Kodi ukanamanga motani Nyumba Yaufumu? Oimira mpingo wapamalopo anapempha kusamutsira kumalo ena chipatalacho ndi kusafuna kulipiridwa. Kodi Yehova akatsogolera zinthuzo motani? Mbiri yokondweretsa! Pempho lawo linavomerezedwa!

Tsopano tiyeni pankhani inayo​—malo a nyumbayo. Inde, iwo anauzidwa kuti, kunawonekera ngati kuti malo aboma angaperekedwe mwaulere, malinga ngati nyumbayo idzasungidwa monga momwe iriri ndi kubwezeretsedwa. Komabe, pofika panthaŵiyi chitsutso cha ntchito yolingaliridwayo chinali kukula kuchigawo china chopanda ubwenzi cha chitaganyacho. Chikalata cha pempho chinakonzedwa chimene chinalinganizidwira kuimitsa mapulani a Mbonizo. Mphekesera zakuti Mboni za Yehova zikatenga Cooktown, kutseka mahotela ndi malo otchoverako juga, ndi kuletsa kugulitsidwa kwa fodya zinafalitsidwa. Ndithudi, zimenezi sizinachitike, koma kupeza kusinthidwa kwa malowo ndi kupeza chivomerezo chofunika cha nyumbayo zinakhala zovuta kwambiri. Tsiku lake lotsiriza losamutsa nyumbayo linali kuyandikira mofulumira. Kuloŵeramo kwa Boma la Queensland kunapemphedwa. (Yerekezerani ndi Aroma 13:2.) Chilolezo cha kugwiritsira ntchito malo a bomawo chinaperekedwa mwamsanga, ndiponso chilolezo cha nyumbayo chinaperekedwa. Pokhala ndi zonse ziŵiri malo ndi nyumbayo m’manja mwawo, nchiyanino chinatsatira?

Ndiyeno panadza kagulu ka mazana a Mboni, amisiri odziŵa ntchito zawo ndi owathandiza kuchokera kumbali zosiyanasiyana za Boma la Queensland, amene amapatula nthaŵi yawo kukatumikira modzifunira ndipo akulitsa luso la kumanga Nyumba Zaufumu mwamsanga. Ntchito imeneyi inapereka zitokoso zapadera: kusamutsa zipupa za chipatala cha zipinda ziŵiri zosanja kumka nazo kumalo atsopano ndiyeno kukaimikanso nyumbayo. Nyengo ya mkuntho wamvula inali kuyandikira mwamsanga, ikumachititsa kuwopseza kwa mvula yamkuntho. Kodi ntchitoyo ikatha panthaŵi yake? Anthu ena a m’tauniyo anakayikira. Komabe, chimene chinawonekera kwa ena kukhala chosatheka mwamsanga chinatsirizidwa. Mu April 1986 nyumbayo inasamutsidwa ndipo pambuyo pake inabwezeretsedwa kuulemerero wake wapoyamba.

Ntchito yonseyi sinachitidwe mosawonedwa, monga momwe zikusonyezera ndemanga za mu Anglican Newsletter ya mu Cooktown. Mwapang’ono iyo inati: “Mosakayikira ndikasulizidwa, komano . . . tayang’anani pa Tchalitchipo ndi kuwona kusadzaza kwake ndi anthu ndipo yang’ananinso pakagulu ka anthuko [Mboni za Yehova] ndi kuwona mmene akudzadzira . . . , ndi Aangilikani ndi Akatolika . . . Kodi mumadziŵa kuti gulu lina . . . [lagula] Chipatala chakale chija ndi kuchimanganso m’chimene angachitche kuti tchalitchi chifukwa chakuti Sukulu imene amachitirako misonkhano njaing’ono kwambiri kuti onsewo asonkhanemo? . . . Takhala ofooka chotani nanga, kulola zimenezi kuchitika.”

Zikwi za anthu owona malo zimafika m’Cooktown chaka chirichonse. Iwo amadza kudzasangalala ndi nkhalango yobiriŵira yokongola ndi Great Barrier Reef ndi kuphunzira za mbiri ya deralo. Myuziyamu ya Captain Cook ndiyo chochititsa chidwi chotchuka kwa odzawona ochuluka. Chiyambire 1989 Chipatala cha Cooktown chotchukacho m’ntchito yake yatsopano monga Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova chakhalanso chokopa chachikulu cha odzacheza. Masitolo ake ogulitsa zinthu zazikumbukiro zake amagulitsanso mathawulo a tii ndi masikipa amene ali odindidwa ndi chithunzithunzi cha Chipatala cha Cooktown ndi Nyumba Yaufumu. Mkati mwa nyengo ya alendo, pakati pa anthu mazana asanu ndi limodzi ndi chikwi amafika panyumbayo mlungu uliwonse kudzaziwonera mamangidwe ake apadera a 1879.

Magazini amene tsopano akutchedwa Nsanja ya Olonda amapezeka mwaulere kwa odzayendawo. Kuyambira mu 1879 magazini ameneŵa awonjezeka kufalitsidwa kwake kufikira pamakope oposa mamiliyoni 15 kaŵiri pamwezi m’zinenero 111. Amasonyeza anthu paokha lonjezo la Baibulo lakuti ena a mbadwo wa 1914 adzakhalabe amoyo kudzawona thanzi lakuthupi ndi lauzimu labwino zikumabwezeretsedwa kwa anthu. (Yesaya 33:24) Dziko lonse lapansi lidzasandulizidwa kukhala paradaiso ndi mamiliyoni a odzipereka kutero. (Salmo 37:29) Bwanji osafika pa Nyumba Yaufumu ya m’dera lanu? Mudzapeza kanthu kena kamtengo wapatali koposa golidi yense amene anakumbidwapo m’chigawo cha Cooktown.​—Miyambo 16:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena