Lipoti la Olengeza Ufumu
Mbiri Yabwino Yochokera ku Yuropu Wakum’maŵa
ZINTHU zambiri zochititsa chidwi zikuchitika m’munda wateokratiki wa ku Yuropu Wakum’maŵa. Chapadera chinali msonkhano wamitundu yonse mu Zagreb, August 16-18, 1991, kumene Mboni zokwanira 7,300 zinalandira mwachikondi abale awo ochokera kumaiko 15. Onse pamodzi, okwanira 14,684 anafikapo. Chinali chisonyezero chodabwitsa cha chikondi ndi umodzi m’dzikolo lokanthidwa ndi chipoloŵe!
Mboni za ku Yuropu Wakum’maŵa nzotanganitsidwa kuuza ena za mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova, umene zimauzindikira kukhala chiyembekezo chokha cha mtendere weniweni. M’madera ena kumakhaladi kovuta kusunga kaimidwe kawo kauchete. Chikhalirechobe, anthu kaŵirikaŵiri amamvetsera, ndipo Mbonizo zimasimba zokumana nazo zabwino zambiri.
Mu tauni lina, msungwana wazaka 16 anamva mbiri yabwino kwa Mboni imodzi yokha ya Yehova m’taunilo. Phunziro la Baibulo lokhazikika linayambidwa, ndipo chiyamikiro chake cha chowonadi chinakula. Pokhala ndi chikhumbo chachikulu chakufuna kuuza ena zinthu zodabwitsa zimene anaphunzira, msungwanayo anayesa kulankhula ndi anzake apasukulu koma anamtsutsa ndi kumseka. Panali mnzake wina wapasukulu amene anamtsutsa kwambiri koma anadabwa ndi kuchita chidwi ndi kuleza mtima kwake, popeza kuti wophunzira Baibulo wachichepereyo sanakwiye ngakhale kuti ananyodoledwa kwambiri. Pambuyo pake, umboni wogwira mtima kwambiri unaperekedwa kwa msungwana ameneyu, ndipo anazindikira kuti kaimidwe kake kamaganizo kanali kolakwa. Phunziro la Baibulo linayambidwa naye, ndiyeno wophunzira Baibulo woyambayo ndi bwenzi lake latsopanolo anayesayesa kugaŵana chimwemwe chawo ndi ena, mosasamala kanthu za chitsutso cha makolo awo, mphunzitsi wawo, ndi anzawo apasukulu.
Monga chotulukapo cha kuchitira umboni kwawo, mnzawo winanso wapasukulu anavomereza chowonadi. Tsopano anali atatu m’kalasi lawo, ndipo atatu onsewo anali ndi chitsanzo chabwino chakufunitsitsa kuthandiza ena ndi kusonyeza chikondi pakati pawo. Pamenepo msungwana wina anagwirizana nawo.
Tsopano anali kukhala anayi pabentchi yapabwalo lasukulu pokambitsirana Baibulo. Ndipo ambiri anadabwa kuwona kuti chiŵerengero chawo chinakula. Msungwana wina wa m’kalasiyo, amene anachita chidwi ndi mkhalidwe wawo wabwino, anasankha kutsagana nawo m’phunziro la Baibulo. Asanuwo anapitiriza kuitanirabe ena, ophunzira ndi aphunzitsi, kuti achite chimodzimodzi. Komabe, asungwanawo anapitirizabe kuvutitsidwa ndi makolo awo. Makolowo anayesa mwamphamvu kukakamiza asungwanawo kuleka phunziro lawo la Baibulo mwakuwononga mabuku awo ndi kuwachitira nkhanza.
Kodi chotulukapo chinali chotani cha kuchitira umboni kumeneku koyambidwa ndi wokondwerera wachichepere mmodzi? Mmodzi wa asungwanawo anabatizidwa pamsonkhano wachigawo mu 1990, ndipo anayi enawo pamsonkhano wadera m’chirimwe cha 1991. Izi zinali zodzetsa chisangalalo chachikulu! Lerolino, asungwana onse asanu akutumikira monga apainiya okhazikika! M’tauni limene zimenezi zinachitikira, tsopano muli ofalitsa 11, ndipo 8 mwa ameneŵa ali muutumiki waupainiya.
Yehova akuchirikiza ndi kudalitsa Mboni zake mu Yuropu Wakum’maŵa. Mwachiwonekere pali kuthekera kwakukulu kwa chiwonjezeko pakati pa anthu owona mtima m’mbali imeneyi yadziko.