Agibeoni—Anafuna Mtendere
MZINDA womwe uli pamwamba paphiriwo pamwambapa ukunenedwa kuti uli pamalo omwe Gibeoni wakale anali, makilomita 10 kumpoto kwa Yerusalemu.
Mwinamwake mukudziŵa kuti Gibeoni anatchuka kwambiri mwamsanga pambuyo pakuti Yoswa anatsogolera Israyeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa ndi kugonjetsa Yeriko. Akanani a ku Gibeoni anazindikira kuti sangalake Israyeli, yemwe mosakaikira anali ndi chilikizo la Mulungu. Kodi anayenera kuchitanji? Mwakugwiritsira ntchito machenjera, Agibeoni anatumiza mithenga yomwe inadzisonyeza ngati alendo ochokera kudziko lakutali. Zoyesayesa zofuna mtendere zimenezi zinapambana, popeza kuti Israyeli anachita nawo pangano. Pamene machenjera awo anaululika, Agibeoni anakhala otema nkhuni ndi otunga madzi.
Mulungu sanaipidwe ndi anthu aŵa amene anafuna mtendere. Iye anachilikiza Yoswa kuchinjiriza Agibeoni pamene anaukiridwa ndi mafumu asanu. Yehova anachitadi chozizwitsa chakutalikitsa usana pankhondoyo.—Yoswa 9:3-27; 10:1-14.
Pachitunda chimenechi ofukula anapezapo dzenje lakuya, kapena thamanda, lokumbidwa m’thanthwe lolimba. Agibeoni ankatsika masitepe kukatunga madzi ochokera pansi. Kodi limeneli lingakhale “thamanda la Gibeoni” lotchulidwa pa 2 Samueli 2:13? Ofukula za m’mabwinja anapezanso nkhokwe zokumbidwa m’thanthwe ndi ziŵiya zambiri zopangira vinyo. Inde, kukuwonekera kuti Gibeoni anali malo apakati opangira vinyo.
M’nthaŵi ya Davide, chihema, kapena kachisi wa Mulungu wowona anali kumeneko. Mfumu Solomo anadza kuno kudzapereka nsembe. Yehova anawonekera kwa Solomo m’kulota ndipo anamlonjeza “mtima wanzeru ndi wakuzindikira,” limodzinso ndi chuma. (1 Mafumu 3:4-14; 2 Mbiri 1:3) Nkhani ya pamasamba 12-17 a kope lino ikusonyeza kuti mbadwa za anthu amene anakhala ku Gibeoni anali ndi mwaŵi wapadera pakati pa mtundu wa Mulungu panthaŵi ina yakutsogolo. Kodi mukudziŵa kuti unachitika motani?
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.