Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 3/1 tsamba 32
  • “Mboni za Yehova?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mboni za Yehova?”
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 3/1 tsamba 32

“Mboni za Yehova?”

FUNSO liri pamwambali linali mutu wankhani mu Bulletin of the University of Helsinki, magazini a chinenero cha Chifinish. Pansi pa mutuwo Profesa Jorma Palo analembapo kalata imene mbali yake inati: “Ndinapenda mosamalitsa chizindikiro cha yunivesiti yathu chosindikizidwa pachikuto cha magazini a Bulletin. Chapamwamba pake, ndinapeza zilembo za Chihebri ndipo ndinafunsa tanthauzo lake kwa mlendo wanga Myuda. Malinga ndi katswiri ameneyu, wodziŵa Chihebri, liwulo ndilo ‘Yehova’ m’Chifinish.”

Kupezeka kwa dzina laumwini la Mulungu pachizindikiro cha yunivesiti ya ku Finland kunadabwitsa ena. Ngakhale nditero, yunivesitiyo yakhala zaka 350, ndipo pamene inakhazikitsidwa, dzina la Yehova linali lodziŵika kwambiri ndipo linkagwiritsiridwa ntchito mu Yuropu yense. Dzinalo limapezeka panyumba zaboma zosaŵerengeka, pamakobiri, ndi pazizindikiro zosonyeza deti lanyengoyo.​—Onani brosha ya Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha.

M’zaka za zana lino, Chikristu Chadziko sichimaligwiritsiranso ntchito dzina la Mulungu, ndipo chikondwerero choyambirira padzinalo chaiŵalika kotheratu. Gulu limodzi lokha ndilo limagwiritsira ntchito dzina la Mulungulo ndi kulifalitsa ponseponse, mogwirizana ndi pempho loyamba m’Pemphero la Ambuye lakuti: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’ (Mateyu 6:9) Chifukwa chake, pamene dzinalo linadziŵika pachizindikiro cha yunivesiti, anthu panthaŵi yomweyo anakumbukira Mboni za Yehova.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Yliopisto

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena