Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Yenderani Dzikolo, Yenderaninso Nkhosa!
AKRISTU zikwi zambiri apita kukayendera Dziko Lolonjezedwa, akumaganiza kuti kuwona malo kumene zinthu zinachitikira kudzaŵathandiza kumvetsetsa Baibulo, kulipangitsa kukhala latanthauzo kwambiri. Ndipo zakhaladi tero.
Kaya ngati munayenderapo malowo m’lingaliro lenileni kapena mwamaganizo mwakuŵerenga mabuku ndi nkhani zonena za dzikolo, kodi munaziyenderapo nkhosa? ‘Kodi nkhosa zinali ndi mbali yanji m’Dziko Lolonjezedwa?’ mungafunse motero. Kwenikweni, nkhosa zinali mbali yaikulu ya moyo wa m’nthaŵi za Baibulo kwakuti kuyendera Dziko Lolonjezedwa popanda kuyendera nkhosa nkosakwanira m’lingaliro lina.
Zithunzithunzi zimene mukuwona panopa mungaziwone pakuyendera kwanu, pakuti nkhosa zimene mukhoza kuwona m’deralo lerolino nzofanana kwambiri ndi zija zofala m’nyengo ya Baibulo.a Michira yawo yaikuluyo njolemera ndi mafuta. (Levitiko 7:3; 9:19) Kaŵirikaŵiri ubweya wochulukawo ngoyera. Koma kumbukirani kuti gulu lankhosa lalikulu la Yakobo linali ndi ‘zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga.’—Genesis 30:32.
Cholembedwa chimenechi chimasonyeza kuti munthu amene anali ndi nkhosa zambiri analingaliridwa kukhala wachuma. (Genesis 30:43) Timaŵerenga za Yobu kuti: ‘Zoŵeta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziŵiri, ndi ngamila zikwi zitatu, ndi ng’ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu akazi mazana asanu . . . [Iye] anaposa anthu onse a Kum’maŵa.’ (Yobu 1:3; 42:12) Ndiponso kumbukirani kuti Nabala anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Kodi muganiza kuti malo ake ndi chisonkhezero zimene anali nazo m’nthaŵi ya Davide zinali zotani? (1 Samueli 25:2) Koma kodi ndimotani kwenikweni mmene nkhosa zambiri zinaliri chuma chochuluka?
Chifukwa chakuti nkhosazo zinapatsa mbusa wawo kapena mwini wake zinthu zamtengo wake. Ubweya weniweniwo unali chuma chomabwererapo mwakukulanso. Miyambo 31:13, 21, 22 imatithandiza kuwona mmene mkazi wanzeru ndi waufulu ankagwiritsirira ntchito ubweyawo kupangira banja lake malaya kapena zofunda zokagulitsa. (Yobu 31:20) Ubweya unali katundu wofunika wamalonda. Mfundoyo ikuwonedwa m’mawu akuti mfumu ya Moabu ‘inali mwini nkhosa, ikapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi [nkhosa zamphongo zosasenga, NW] zana limodzi.’ (2 Mafumu 3:4) Inde, zinali nkhosa “zosasenga”; ubweya wawo wochulukawo unawonjezera mtengo wawo.
Nkhosa zamphongo, zinali ndi nyanga zokomeza, monga zomwe zili pachithunzithunzi kulamanja. Kodi zimenezi zimakukumbutsani kuti nyanga ya nkhosa yamphongo inkagwiritsiridwa ntchito kulengezera Chaka Choliza Lipenga? (Levitiko 25:8-10) Nyanga zofanana zamphako zinkagwiritsiridwa ntchito kuchenjezera tsoka kapena pomenya nkhondo.—Oweruza 6:34; 7:18, 19; Yoweli 2:1.
Moyenerera, ngati munali ndi gulu lankhosa, simukanasoŵa chakudya chifukwa chakuti nkhosa zinali pakati pa zinyama zimene Aisrayeli analoledwa kudya. (Deuteronomo 14:4) Nyama (yankhosa) inkaphikidwa kapena kuwotchedwa. Nkhosa yowotcha inali chinthu chachikulu paphwando lapachaka la Paskha. (Eksodo 12:3-9) Nkhosa zinalinso magwero a mkaka, womwe unkamwedwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kupangira tchizi.—1 Samueli 17:17, 18; Yobu 10:10; Yesaya 7:21, 22.
Kuyendera nkhosako sikukakwanira popanda kuwona unansi wathithithi pakati pa gulu lankhosalo ndi mbusa wake. Mbusa wokhulupirika ankazisamalira bwino nkhosa zake. Monga momwe ananenera Yesu, zikazindikira mawu a mbusa wawo ndi kulabadira ataziitana ndi dzina. (Yohane 10:3, 4) Ina itasokera, mbusa wachikondiyo akapita kukaifunafuna. Ataipeza nkhosa yosokerayo, mwina akainyamulira pamapeŵa pake naibweza kwa zinzake.—Luka 15:4, 5.
Davide anagwiritsira ntchito ubusa wake wankhosa pamene anadzifananitsa ndi nkhosa yokhala ndi Yehova monga Mbusa wake. Davide anachinjirizidwa, monga momwe nkhosa zinatetezeredwa ku zinyama zolusa. Nkhosazo zikatsatira chitsogozo cha mbusa wawo wodera nkhaŵa. Zitavulala, ankatsuka ndi kumangapo pamabalapo, mwinamwake ndi mafuta opha ululu. Ha, zimenezi nzosiyana chotani nanga ndi zochita zaumbombo za atsogoleri a Israyeli, ofotokozedwa pa Ezekieli 34:3-8!
Baibulo limatchula nkhosa m’mawu ochuluka ophiphiritsira ndi aulosi. Choncho kuyendera kwanu, kozidziŵa bwino nkhosa za ku Dziko Lolonjezedwa, kungazamitse kumvetsetsa kwanu mawu akuti “kagulu ka nkhosa,” “Mwanawankhosa wa Mulungu,” ndi “nkhosa zina.”—Luka 12:32; Yohane 1:36; 10:16.
[Mawu a M’munsi]
a Chithunzithunzi chomwe chiri pamwamba, cha nkhosa m’chipululu cha Yudeya mukhoza kuchipenda pa Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1992.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Garo Nalbandian