Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/15 tsamba 31
  • Chiukiriro cha m’Mzaka Chikwi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiukiriro cha m’Mzaka Chikwi
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/15 tsamba 31

Chiukiriro cha m’Mzaka Chikwi

CHIŴERENGERO choyerekezera kwambiri cha anthu amene akhalapo padziko lapansi ndi 20 biliyoni. Ambiri ofufuza nkhani imeneyi aŵerengera kuti sianthu ambiri choncho amene akhalapo padziko lapansi. Sikuti onseŵa adzaukitsidwa, koma ngakhale titayerekezera kuti akatero, sipakakhalabe vuto lirilonse ponena za malo okhala kapena chakudya. Ukulu wa malo adziko lapansi pakali pano ngokwanira pafupifupi makilomita 148,000,000 mbali zonse zinayi, kapena pafupifupi mahekitala 14,800,000,000. Ngakhale ngati theka la malo ameneŵa lingapatulidwe kaamba ka zifuno zina, munthu aliyense akhoza kulandirabe malo oposa chigawo chimodzi mwa zitatu cha hekitala. Ponena za mphamvu yakubala zakudya ya dziko lapansi, kwenikweni chigawo chimodzi mwa zitatu cha hekitala chidzapereka chakudya chimene munthu mmodzi sadzachitha, makamaka poti padzakhala chakudya cha mwana alirenji chifukwa cha dalitso la Mulungu, monga anachitira chitsanzo kwa mtundu wa Israyeli.​—1 Mafumu 4:20; Ezekieli 34:27.

Ponena za mphamvu yakubala chakudya ya dziko lapansi, United Nations Food and Agriculture Organization imanena kuti, mwakungowongolera pang’ono njira zamalimidwe, ngakhale m’maiko osatukuka, dziko lapansi likhoza kudyetsa mosavuta chiŵerengero cha anthu chimene asayansi achiyerekezera kuti chidzakhalapo m’chaka cha 2000 kuchiŵirikiza kasanu ndi kanayi.​—Land, Food and People, Rome, 1984, masamba 16, 17.

Komabe, kodi mamiliyoni zikwizikwi amenewo adzasamaliridwa motani, polingalira chenicheni chakuti kalelo ambiri a iwo sadamdziŵe Mulungu ndipo adzayenera kuphunzira kusunga malamulo ake? Choyamba, Baibulo limanena kuti ufumu wa dziko ukhala ‘wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake, ndipo [adzalamulira] monga mfumu kufikira nthaŵi zanthaŵi.’ (Chivumbulutso 11:15) Ndipo chiphunzitso cha Baibulo nchakuti ‘pamene maweruziro anu [Yehova] ali padziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.’ (Yesaya 26:9) Panthaŵi yake yoyenera, pamene kudzakhala kofunika kudziŵitsa atumiki ake, Mulungu adzavumbula mmene adzasamalirira ntchito yake.​—Amosi 3:7.

Kuchitira fanizo kudzasonyeza kuti makonzedwe a Yehova kulinga kwa mtundu wa anthu ali nkhani yapafupi kwa iye. Osati kuti nkulosera, koma kungofotokoza mwafanizo, tiyeni tiyerekezere kuti awo amene ali a ‘khamu lalikulu’ la anthu olungama amene ‘akutuluka m’chisautso chachikulu’ m’dongosolo lazinthu lilipoli amoyo (Chivumbulutso 7:9, 14) ali okwanira 3,000,000 (pafupifupi 1/1666 ya chiŵerengero cha anthu padziko pakali pano). Ndiyeno, ngati pambuyo poŵapatsa, tinene kuti zaka 100, zakuti aphunzitsidwe ndi ‘kugonjetsa’ gawo la dziko lapansi (Genesis 1:28), Mulungu aukitsa maperesenti atatu a chiŵerengero chimenechi, chikatanthauza kuti munthu aliyense wobwera chatsopano akasamaliridwa ndi anthu 33 ophunzitsidwa. Popeza kuti chiwonjezeko chapachaka cha maperesenti atatu, chophatikizidwa pamodzi, chimaŵirikiza chiŵerengerochi kaŵiri pambuyo pa zaka 24 zirizonse, anthu onse 20 biliyoni akhoza kuukitsidwa zisanathe zaka 400 za Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, kusiyako nthaŵi yokwanira yakuphunzitsa ndi kuweruza oukitsidwawo popanda kudodometsa chigwirizano ndi dongosolo padziko lapansi. Chotero Mulungu, ndi mphamvu yake yopambana ndi nzeru, ali wokhoza kukwaniritsa chifuno chake mwaulemerero mosalakwira malamulo ake ndi makonzedwe amene waika kaamba ka mtundu wa anthu kuyambira pachiyambi, kuwonjezerapo chisomo chake cha chiukiriro.​—Aroma 11:33-36.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena