Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/15 tsamba 29
  • Kubwezeretsedwa kwa Dzina la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwezeretsedwa kwa Dzina la Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/15 tsamba 29

Kubwezeretsedwa kwa Dzina la Mulungu

“PAPITA pafupifupi zaka 60 kuti dzina la Mulungu, ‘JHWH,’ amene ali Mulungu osati wa Ayuda okha komanso wa Akristu, liikidwenso pamene wopaka utoto analiika poyambirira.” Ndimmene nyuzipepala ya ku Jeremani ya Schwarzwälder Bote inanenera za kubwezeretsedwa kwa dzina la Mulungu pakhoma la holo yamzinda ku Horb, kum’mwera kwa Jeremani. Koma kodi nchifukwa ninji dzinalo linachotsedwa?

Nyuzipepalayo inasimba kuti kunja kwa holo yamzinda kunajambulidwa zithuzithuzi zokometsera khomalo zochititsa kaso. Zinaphatikizapo Tetragrammaton, zilembo zinayi Zachihebri za dzina la Mulungu.

“Dzinali, limene limapezeka m’Baibulo zoposa nthaŵi 6,000,” inatero nyuzipepalayo, “ndilo ‘Jehova’ kapena lina lofanana nalo m’Chijeremani. Matchulidwe enieni ngosadziŵika bwino chifukwa chakuti Chihebri chinali ndi makonsonanti okhaokha. Mavaulo ankaikidwamo ndi woŵerenga.”

Komabe, mu 1934 oimira Chipani cha Nazi anawona kuti Tetragrammaton inali “yosayenererana ndi nthanthi yamakono” choncho anaifafaniza ndi utoto. Mwachimwemwe, Tetragrammaton inabwezeretsedwa. Nyuzipepalayo inanena kuti: “Lerolino khoma la [holo yamzinda], lokometseredwa ndi zithunzithunzi za m’mbiri, zizindikiro zodziŵira fuko kapena tauni, ndi zithunzithunzi za anthu, ndilo ‘malo’ amene munthu sayenera kuphonya kuwawona ku Horb.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena