Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/1 tsamba 31
  • Iwo Amachita Zimene Angathe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iwo Amachita Zimene Angathe
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • “Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupereka kwa Amene Ali ndi Chilichonse?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • ‘Muziika Kenakake Pambali’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/1 tsamba 31

Iwo Amachita Zimene Angathe

Ngakhale kuti sali okhoza kumbwezera Yehova kaamba ka zabwino zake zonse kwa iwo, ambiri amachita zimene angathe kuchirikiza ntchito yolalikira yapadziko lonse ya Mboni zake. (Mateyu 24:14; yerekezerani ndi Marko 14:3-9.) Kalata iyi yochokera ku banja la ku Minnesota, U.S.A. iri yosangalatsa:

“Abale Okondedwa,

“Tikutumiza chopereka cha unyinji wa $​——. Tikupempha kuti chigwiritsiridwe ntchito kulipirira ntchito yapadziko lonse kapena kuperekedwa ku Thumba la Ndalama za Nyumba Yaufumu, kapena ku chosoŵa china chirichonse chimene gulu lingakhale nacho. . . .

“Ndife achidaliro kuti ndalamazi zidzagwiritsiridwa ntchito mogwirizana ndi chifuniro cha [Yehova]. Tingakonde kugwiritsira ntchito mwaŵiwu kukulimbikitsani kupitiriza ntchito yabwinoyi, ndipo makamaka tikuthokozani chifukwa cha “videotape” ya kagwiridwe ka ntchito ka padziko lonse ka [Watch Tower] Society. Inali tepi imeneyi imene inatizindikiritsa za ntchito yaikuluyo, ndipo inakhomereza m’maganizo mwathu kuti zopereka zathu zodzifunira zimafunidwa. Kalelo, tinalekera mpingo, dera, ndi chigawo kusamalira zokutumizirani zopereka, koma tsopano tikuthokoza Yehova chifukwa chokhala woleza mtima ndi kusawona patali kwathu ndikutisonyeza mwachikondi kufunika kwa kuthandiza mwaumwini kulipirira ntchito yopulumutsa moyoyi, kuwonjezera pa zopereka zina. Monga banja, tamvana kumatumiza mwachindunji ku New York unyinji wosachepera wa $​——​pamwezi.

“Kachiŵirinso, tikuthokozani kaamba ka utumiki wabwino umene mumatichitira ndi kukhulupirika kwanu kwa Yehova kumene mwakusonyeza.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena